Nkazi Wa Kristu

(Aefeso 5:26-27)


Ambuye amafunitsitsa kuti Mpingo uzizipereka kwa iye ngati nkazi wa iye yekha. Machimo athu anasukidwa kudzera mu ubatizo. Pomvera mau a chipulumutso, zimatifikitsa podalira mphamvu ya Ambuye kufikira kutiyeretsa ku machimo. Kuyeretsedwa uku, komwe kunayamba nthawi yambuyomu, kuyenera kupitilira mpaka tsiku la ulemerero pamene tidzaonekera kwa Ambuye ngati nkazi Wake.

1. Nkazi Woyera
Nkazi wopanda chirema wokondedwa amadzindikirika ndi chiyero? Kodi chiyero ndi ciani? Kodi ndi kukangalika pa ntchito za chipembezo? Okhazikika mu zinthu osati za dziko lapansi? Ozama mu chidziwitso cha chipembezo? Ayi. Monga mwa dongosolo la kuyeretsedwa imakhalira, ndi kuchotsedwa kwa chodetsa kapena zoipa. Nanga chodetsa ndi ciani? Monga kwalembedwa, “Amenewo popeza sazindikiranso kanthu konse, anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite chidetso chonse mwa umbombo.” (AEFESO 4:19, BUKU LOPATULIKA NDILO MAU A MULUNGU) Mu nyengo iyi munthu amakhazikika mu zifooko ndipo amakonda kuchita zodetsa mosongozedwa ndi nsanje.

2. Nkazi Wa Ulemerero
Monga umo mfumu imamuveka nkazi wake zovala zapamwamba ndi zokongoletsa za mtengo wapatali, kuwonetsera mwa nkaziyo za ulemerero wake, momwemonso Ambuye amakhumbira kuonetsera ulemerero wake kudzera ku Mpingo mwa iye yekha. Maonekedwe okongola a nkazi amasimikizira ulemerero wa mfumu kwa anthu onse. Monga umo akhalira mwana obadwa kumene yemwe nkazi wina wamutaya, momwemonso nkazi amazikhazikitsa yekha ndi mtima wonse mokodwera kuchitira umboni za chikondi ndi mphamvu za mfumu populumutsa ndi kumukweza iye. Sakhala okhutira mwa iye yekha kuti wakhala nkazi wa mfumu, Koma kuti tsiku lililonse amayesetsa kuzikongoletsa kuti afikire muyeso omuyenereza kukhala pambali pa mfumu, kapena kuoneka mokongola kusonyeza kuti ndi oyenera kukhala nkazi wa mfumu.

3. Pa Tsiku La Ulemerero
Ngakhale pano, Ambuye akupereka Ulemerero ndi chiyero ku Mpingo. Ngakhale zodetsa ndi zofooka zikuonekabe pakati pathu tsiku ndi tsiku, koma timamukwezabe Ambuye mokondwera ndi kuthokoza. Chifukwa timadziwa kuti mtima Wake unakhazikika pa kukhululukira machimo athu, osati za chilango cha machimo. Ambuye amene tsiku ndi tsiku amavomeleza kulapa ndipo kutitsongolera ndi Mau Ake, ndi mtima onse kufunitsitsa kuti tidzakhale ndi iye pa tsiku la Ulemerero.

Abusa Sung-Hyun Kim 

Malichi 16, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Iye amapereka Mkwatibwi Woyera ndi Waulemerero
Aefeso 5:26-27
Abusa Sung-Hyun Kim