Nkhondo ya Uzimu
(Aefeso 6:10)
Dziko lapansi ndi lodzala ndi mizimu yoipa. Mu ulamuliro wao, anthu sasiya kupanga machimo, zachinyengo, kuperekana mu zoipa, kuukirana, komanso kuononga. Chonsecho muzonsezi mizimu yoipa imabisala osadzionetsera kuti akuchita izi ndi mphamvu ya ziwanda.
1. Madziko a nkhondo zonse
Yesu atalandira Mzimu Woyera, chinthu choyamba kukumana nacho chinali nkhondo ya m’dierekezi. Satana ndi amithenga ake anamva kuwawa kwakukulu ndi kufika kwa Yesu. Choyamba, anayeserera kumuyesa Iye, koma atalephera, anafuna kumupha Iye, ndipo pamapeto pa zonse, Yesu anamupha kudzera mwa anthu omwe anali otsogozedwa ndi ziwanda. Koma anaukanso ku imfa, nakwera ku M’mwamba, ndipo anapepha Atate, motero Mzimu Woyera anaperekedwa – Kudzera mu izi, Mpingo unabadwa.
2. Mpingo uli pa nkhondo
Mpingo waima pakati pa nkhondo ya uzimu. Kwa iwo omwe anapulumutsidwa ndipo ali ziwalo za Mpingo, awa sagwanso mu mabodza a mdierekezi ndi mizimu yoipa. M’malo mwake, amaima motsutsana ndi mphamvu ya tchimo ndi imfa, kudzera mu mphamvu ya Mzimu Woyera. Koma nkhondo za mdierekezi sizitha. Iye ntchito yake sikutseka mitima ya anthu kuti asamve Mau a Mulungu kokha, komanso kuti amapereka mzimu wa mabodza ngakhale mwa okhulupilira – kuwapangitsa kuti apunthwe ndi kuwapotoza kukwanilitsa zokhumba zake. Mapeto ake anthu omwe anaikidwiratu kugwira ntchito ya Mulungu – amagwira ntchito ya mdierekezi.
3. Asilikali a Ambuye
Onse omwe agwira ntchito ya mdierekezi adzaonongedwa ndithu pamodzi ndi iye. Anthu ambiri amadzinamidza okha, nati, ndimakhulupilira mwa Yesu, ndipo ndidzapulumutsidwa, koma Ambuye momveka bwino akunenetsa kuti adzawerudza munthu aliyense molingana ndi ntchito zake. Aliyense angathe kunamidzidwa ndikukhala kapolo wa mdierekezi. Mwa ichi tisakhale ndi chiyembekedzo mwa kuthekera kwa ife tokha, koma tilimbikitsidwe ndi mphamvu ya Kristu. Ndiife asilikali a Ambuye ndipo tili pa nkhondo. Kotero tiime molimba kutsutsana ndi nkhondo ya adani ndi kutetedzera Mpingo.
Abusa Sung-Hyun Kim
8 Juni, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Nkhondo zauzimu ya Mpingo wa Khristu
Aefeso 6:10
Abusa Sung-Hyun Kim