Nkhondo Yosapeweka

(Aefeso 6:10-11)


Mumati mzimu wanu ndiotetezedwe – chifukwa choti ndinu okhulupilira basi? Mumakhala mwa bata – kodi chifukwa mumapewa zolimbana ndi ena? Pali chinthu chimodzi chomwe mukusowa kuchidziwa – mdierekezi sakhala chete. Tili pa nkhondo ndi iye.

1. Njira yoona ya Chipambano
Kwa omwe sanakonzekere bwino ayenera ndithu kugonjetsedwa pa nkhondo iyi. Nanga osakonzekerawo ndi ati? Awa ndi omwe amadalira nzeru ndi mphamvu za iwo okha. Samudziwa mdaniyo – mdierekezi – ndipo sangagonjetse. Pamene mdierekezi waponya zida zake – kulingalira mwapang’ono – “nkumati ndimvesere ndipo kupanga chitsakho mwa ine ndekha” Ichi ndi chitsimikidzo chogonjetsedwa. Kodi munthu payekha ndikotheka kugonjetsa mdierekezi – iye amene anayeserera kugawanitsa Mulungu Atate ndi Mwana wake?

2. Dongosolo la machitidwe a mdierekezi
Monga umo mkango uchitira modekha kusaka nyama kuti udye, mdierekezi amagwira ntchito mozama moti kumakhala kovuta kuzindikira. Pa chifukwa ichi, okhulupilira ambiri sazindikira kuti ali pa nkhondo. Pamene a Israyeli anatuluka mu Aigupto, anaona ndithu zizindikiro ndi zozizwa zomwe Mulungu anachita pakati pao ndi maso awo, koma anabwerera pambuyo mukaphindi kochepa, osati chifukwa anali ozadzidwa ndi ntchito zoipa, koma chifukwa machitidwe a mdierekezi anali amphamvu kwambiri. Iwo amene aweruza chilichonse mwa chidziwitso cha iwo okha, monga modzitukumula, mapeto ake amasandulika kukhala zida za mdierekezi.

3. Lutha la Chipambano
Mumoyo wauzimu – ntchito ya mdierekezi ilibe malire. Ku dziko lonse lapansi – zandale – zachuma – za chikhalidwe – zimayendetsedwa molumikizitsidwa kwa china ndi chinzake –   kutsimikizira dongosolo ndi machitidwe amakono, (zatsopano), tiyenera kudziwa kuti izi zichokera ku mphamvu zauzimu.  Dziko limatchula kuwala chomwe chili mdima, ndipo mdima limati kuunika. Ngakhale pakati pa Akristu – pali kulimbana pa Mpingo – kudzera mu kutathauzira molakwika Mau a Mulungu komanso kupatukira ku zipembedzo zonyenga – izi zikukulirakulira ndithu. Kuti munthu uime mwamphamvu molimbana ndi nkhondo ya mdierekezi, nkoyenera kuvala zida za nkhondo za Mulungu, Iyi ndi nkhondo yokhazikika – Koma Ambuye atigonjetsera kale – Nkhondo yaperekedwa kwa ife ngati mwai oti ifenso tikhale otenga mbali ya chipambano Chake.

Abusa Sung-Hyun Kim 

15 Juni, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Kukhala Moyo Woti Aimire motsutsana ndi Mdyerekezi
Aefeso 6:10-11
Abusa Sung-Hyun Kim