Zoyeneredza kukhala mu Chipambano
(Aefeso 6:12)
‘Mdiereke?, Kwa ine sangachite kanthu, ndimadziwa Baibulo mkati ndi kunja – palibe njira yomwe angathe kundiputsitsa. Ndi anthu okhawo omwe sadziwa choonadi omwe amaopyedwa. Ine? ndine otetedzeka kwathunthu.” Kapena muli mwa m’modzi mwa iwo omwe amalingilira motere? Ngati ndi chomwechi, inu muli mu chiopyedzo chogonjetsedwa pa khondo ndi Mdierekezi – Chifukwa muli ndi khungu kapena simudziwa chimene iye ali.
1. Danga lolimbirana mphamvu
Muyeso wa chikhulupiliro chathu umaima ngati nkhondo pa moyo wathu. Vuto lalikulu ndilo, kuti kulimbana kwathu sikwathupi ndi mwazi. Anthu mwakusadziwa izi, amadzala maganizo mu mitima ya anthu ndi kutakasa malingiliro mwakuthupi m’mitima yao. Zotsatira zake anthu amakhulupilira kuti achita zonse motsogozedwa ndi zolinga za iwo eni – pamene choonadi chake, amakhala kuti apusitsidwa ndi mdierekedzi. Ndipo kumbukirani ichi, Mdierekedzi ndi katswiri odzala kugawanika. Anthu ndi mphamvu zaumunthu sangafikire pa Mdierekezi.
2. Chidziwitso mu chifooko chathu
Nthawi zambiri timakamba za kulimbana kwathu ndi mdierekedzi, koma pa choonadi chake, tikuyenera kuima molimba motsutsana ndi madziko ndi machenjerero a mphamvu imene ilipo – Molingana ndi m’mene alili okhadzikika ndi amphamvu ankhondo ake. Ife anthu timapedzeka kukhala ochepere mphamvu. Onse omwe aganidza kuti ndi okhadzikika mu chitetedzo molimbana ndi mphamvu yake, adzikhadzikitsa okha ngati madziko ofooka a mivi ya mdierekezi. Kuti tigonjetse nkhondo yolimbana ndi mdierekezi, choyambilira mwa zonse ndiko kuvomeledza zofooka zathu, ife eni.
3. Chitsimikidzo cha chigonjetso
Muzonse, sitiyenera kukhala amantha, Ambuye wathu anatigonjetsera kale. Ndi wamphamvu kuposa onse. Ngakhale tili opanda mphamvu mwa ife tokha, ndi mphamvu ya Mulungu, zonse ndi zotheka. Iyi ndi mphamvu yomwe inadzutsa Yesu Kristu kuchokera kwa akufa ndi kumukhadzika Iye pa Mpando waulemerero Kumwamba, ndipo Kumwamba kwakhala nyumba yathu. Nkhondo yathu ndi nkhondo yomwe inagonjetsedwa kale, mwaichi tiyeni tivomeledze zofooka zathu pamene tikuyembekezera Mulungu kuti atipatse kuthekera kopita chitsogolo ndi mphamvu komanso kulimbika, ndi njira yomwe Iye adzatitsogolera.
Abusa Sung-Hyun Kim
22 Juni, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Kumenyana motsutsana ndi Mphamvu Zazikulu Zokonzedwa za Mdani
Aefeso 6:12
Abusa Sung-Hyun Kim


