Chapachifuwa Cha Chilungamo

(Aefeso 6:14)


Omwe abayidwa ndi mivi ya mdierekezi pa chifuwa ndi pa mimba zao amataya kukhulupirika m’mitima, komanso ungwiro wao pomvera Mulungu umagwededzeka. Lingaliro lolapa tchimo pamaso pa Mulungu limakhala kutali – amadzembaitsa Mau a choonadi ndi kudzilungamitsa mwa iwo okha. Malingiliro awo amakhala osakhadzikika – amachimwirabe –  koma m’kati mwao amakhala anthu osatsutsika kapena kuzimvera chisoni – ndipo umunthu wao umawachokera – pamapeto pa zonse ungwiro onse umatha.

1. Chilungamo chodziyeneredza ndi Chilungamo chokhadzikika mu chikhulupiliro pakumvera Mau a Mulungu mwa Kristu Yesu.
Ichi ndi chapachifuwa cha chilungamo chomwe chiyenera kubvalidwa kuti uime molimba kutsutsana ndi machenjerero a mdierekezi. Ichi sichilungamo chodziyeneredza, chilungamo chomwe chimaonetseredwa kudzera mu ntchito zathu, komanso kuthekera kwathu sikungatitetedzere ife ku machenjerero a mdierekezi. Nanga kodi chilungamo chomwe chinakhadzikika mwa chikhulupiliro pa Mau a Mulungu pomvera mwa Yesu Kristu, anasandulika ochimwa chifukwa cha ife? Izi ndizosakwaniranso. Ngakhale kuti chilungamo ichi chinatimasula ku chilango cha tchimo, koma sichili ngati chotchingira kuletsa ntchito zoipa za mdierekezi pa ife.

2. Chilungamo chokhadzikika pa kumvera.
Ndiye ndi mtundu uti wa chilungamo omwe tiyenera kuvala? Ichi ndi chilungamo chomwe chimakhadzikika pamene tamvera ndi kukhulupilira Mau a Mulungu. Chilungamo chomvera ndi mtima onse – Chopanga zinthu zonse motsogodzedwa ndi Mau a Mulungu. Chilungamo chodzitsanthula ndi kudzipereka ku Mau. Kwa okhawo omwe analandira chilungamo chokhadzikika pa chikhulupiriro pa Mau a Mulungu ndi omwe angathe kuyenda mu chilungamo ichi, komanso pamene tili pa chilungamo ichi, sayenera kuchita mwa chidzolowezi kuti basi zonse zili bwino. Ngakhale iwo omwe ali okhulupilira oona mtima sayenera kudziyeneradza kuti anapedza chilungamo chokhadzikika. Kuti tilandire ichi – tiyenera kukhala okhulupirika m’chikhulupiliro kufikira tsiku lomwe tidzakumane ndi Ambuye.

3. Chobvala cha chilungamo choyenera kubvala nthawi zonse.
Pamene nkhondo yayamba – palibe ngakhale m’modzi yemwe amakhala ndi chidziwitso cha malo omwe zida za adani awo ziyenera kugwera. Momwemonso machenjerero a mdierekezi sadziwika kuti afika motani pa munthu. Pachifukwa ichi, chapachifuwa cha chilungamo sichiyenera kubvalidwa mwa nyengo zomwe tikudutsa monga mwa kusanthula Mau mwa kukhumba kwa mitima yathu – koma nthawi zonse – paliponse pomwe tili – muzonse zomwe tikuchita. Tisamadzinamidza m’mitima mwathu ndi kuchita monyalanyadza mosephetsa Mau a Mulungu kufuna kusangalatsa miyoyo yathu. Ngati tichita motero palibenso chifukwa choopa – m’kusawerengera kuti mdierekezi adzidzembaitsa mwakuya motani m’machenjerero ake, ngakhale sizinabvumbulutsidwe kwa ife – Chapachifuwa cha chilungamo chimatitetedzera.

Abusa Sung-Hyun Kim 

6 Julayi, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Valani Chishango cha Chilungamo
Aefeso 6:14
Abusa Sung-Hyun Kim