Nsapato Za Uthenga Wabwino Wa Mtendere
(Aefeso 6:15)
Onse omwe anayanjanitsidwa ndi Mulungu amakhala nthawi zonse olimbika mtima muchigonjetso pa nkhondo ya uzimu. chifukwa amakhulupilira kuti, “Mulungu amandikonda, Iye sadzandisiya, Iye amandimenyera nkhondo.”
1. Nsapato za msilikali.
Uku ndi kulimbika mtima kwa msilikali podzibveka nsapato zoyenera molingana ndi khondoyo. Ngati chopondera chapansi cha nsapatoyo chili chosalimba molinga ndi ncthito yake, mkati mwake mumakhala kusinkhasikha , pamene adutsa mutchire, kupunthwa ku zinthu monga miyala. Nsapatoyo itha kubvuka ndithu, kotero sangathe kumenya nkhondo ndi mtima onse molimba. Munjira ina, ngati wadzibveka nsapato zoyenera molingana ndi nkhondoyo – Ichi chimakhala chinthu china chopereka chilimbikitso cha chipambano. Ichi ndi chifukwa chake Ambuye anatilamulira ife. “Ndipo mutadzibveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere.”
2. Kuyanjanitsidwa ndi Mulungu.
“Uthenga wabwino wa mtendere,” siutanthauza kuti ndi uthenga omwe umapereka chitothozo ku moya wakuthupi okha, “Apa, “Mtendere” Zikutanthauza za ubale omwe unaduka ndi Mulungu omwe wayanjanitsidwanso kudzera mu nsembe ya Kristu. Mulungu sakodwera ndi tchimo. Pakanapanda kukoma mtima kwa Kristu, pamene taima motsutsana ndi Iye, akanatha kutiononga chifukwa cha kuopsya kwa mkwiyo wache pa tchimo. Koma chilango ichi chinaperekedwa kwa Kristu pa mtanda. Ndipo chilango chachikulu chinachotsedwa kwa ife. Uku ndiko kuyanjanitsidwa komwe Uthenga Wabwino wabweretsa kwa ife.
3. Kulapa ndi zipatso zake.
Kuti tipedze chikondwerero pa kuyanjanitsidwa, tiyenera kumvera Uthenga Wabwino ndi kulapa. Onse omwe analapa kwatunthu amakhala moyo owonetsera kukonzeka kwa m’mitima yao moyo wao onse. monga umo msilikali nthawi zonse adzibveka nsapato kukonzekera nkhondo iliyonse – yomwe itha kufika nthawi iliyonse. Izi sizitanthauza kumvetsera tchimo lililonse lomwe tinachita – kapena kudziyeneredza kukhala wolungama chonsecho tinagwa kale pa tchimo. Chibadwidwe chathu chinagwa kale ku tchimo. Izi tiyenera kudzibvomeredza ndithu ndipo tipange chisankho chosintha kufuna moyo. Omwe amalapa motero amakhala anthu okondwera – kuposa zonse – Kuyanjanitsidwa ndi Mpingo komanso ndi okhulupilira anzathu. Ichi ndi chitsimikidzo choona choonetsera kuti anayanjanitsidwa ndi Mulungu.
Abusa Sung-Hyun Kim
13 Julayi, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Nsapato Za Uthenga Wabwino Wa Mtendere
Aefeso 6:15
Abusa Sung-Hyun Kim


