Pemphero
(Aefeso 6:18)
Pemphero limapereka kuthekera kuti zida za asilikali a nkhondo ya uzimu zigwire ntchito yake moyenera, chifukwa akhristu omwe amakumana ndi machenjerero akulu a m’dani mu khondo iyi – pemphero – munjira ina iliyonse – siliyenera kudulidwa.
1. Mwa Mzimu.
Pemphero liyenera kuperekedwa “mwa Mzimu”. Nthawi zambiri timati timapemphera “mwa Mzimu” koma kuyankhula kotere kumapereka maganizo omutenga Iye ngati chida kapena kuthekera kopedzera zinthu zina, Ngati tikhadzikika mu lingaliro ngati ili, tingathe kugwa mu chiophyezo chomutenga Mzimu ngati mphamvu kapena nthandizi – ogwilitsidwa ntchito pa zinthu zomwe ife tikukhumba. Kupemphera “mwa Mzimu” ndiko kulinganidza maganizo ndi cholinga kukhala zomangililana ndi kukhadzikika mu zomwe zili mu pemphero zomwe Mzimu amadzipereka. Omwe amapemphera munjira yotere sagwilitsa ntchito mphamvu ya Mzimu kukwanilitsa zokhumba za matupi awo, m’malo mwake, amabvomeredza kuti Iye ndi wamphamvuzonse ndipo amadzipereka mwaiwo okha kwa Iye.
2. Mwa chipiliro chonse.
Kulamulira kuti, “chezerani” ndi kupemphera sizitanthauza kuti tichepetse nthawi yathu yogona usiku ndi cholinga choti tipemphere. Ngati mitima yathu yamangilirika ndi zinthu za dziko lapansi ndi kusatira zinthu zopanda pake, nkosatheka kupemphera mu choonadi. Tiyenera kupempherera zosowa za uzimu, ngakhale kuti yankho lathu silikubwera mwachangu, sitiyenera kudukidza koma kupemphera “mwa chipiliro chonse” . Tisamadera nkhawa, pemphero loperekedwa molingana ndi zofuna za Mulungu limafikadi kwa Iye – ndipo tiyenera kupitilidza mosalekedza kufikira yankho la pemphero lathu litabvumbulutsidwa.
3. Kwa Mpingo.
Ngati talandiradi cholowa cha Kumwamba, Pemphero lomwe tikuyenera kukhadzikikapo koyambilira pa dziko lapansi pano liyenera kukhala lolimbana ndi nkhondo ya uzimu. Nthawi zina “Pemphero kwa Mpingo” sitipemphera monga mwa chisankho cha mtima wathu, koma uwu ndi udindo kwa iwo omwe anaitanidwa ngati ziwalo za Mpingo. Tiyeni tipempherere okhulupilira onse kuti agonjetse machenjerero onse a m’dani, ndi kuyang’anira za chipambano chomwe Ambuye anatipatsa ife. Pemphero longa ili lili ngati chitsimikidzo cha mphamvu yotisimikidzira kuti taima pa chisomo chachikulu cha Mulungu. Ngakhale lero, tilumikidzidwe mitima yathu kuima pamodzi – kutengapo udindo pa Mpingo – monga dera la tsogolo lathu la muyaya mu uzimu.
Abusa Sung-Hyun Kim
10 Ogasiti, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Pempherani Mpingo
Aefeso 6:18
Abusa Sung-Hyun Kim



