KAPOLO WA YESU KRISTU

(Aroma 1:1)


Mtumiki Paulo anali okhadzikika mu maphunziro komanso mu nzeru zakuya. Anali ndi zomuyeneredza kukhala nzika ya dziko la Roma, anakhala pa chiphunzitso pansi pa mphuzitsi wamkulu odziwika ndi dzina loti Gamaliyeli, ndipo anali m’modzi mwa atumwi khumi ndi atatu a padziko lapansi amene anaitanidwa ndi mwini wake Yesu Kristu oukitsidwa ku imfa, mwa iye yekha mwa chindunji.  Koma pamene akudzionetsera yekha kwa okhulupilira ku Roma, anasankha kudzitchura kuti , “kapolo wa Yesu Kristu.”

1. Kapolo odzichepetsa

Paulo monga munthu samadziona mwa ulemerero omwe uli mu Chipangano Chakale omwe uti, “Mtumiki wa Mulungu,” koma mwakukhumba kwa mtima wake anadzionesera ku ulamuliro woyamba wa Aroma ngati kapolo odzicheptsa. Munthawi iyi kapolo anali ngati umo akhalira katundu kwa mbuye wake, analibe ufulu ulionse wa chibadwidwe . Paulo amadziyankhulira yekha ngati “otumikira” (operekera chakudya pa gome) komanso ngati ‘wantchito’ (onga ngati munthu wapansi pa onse opembedza) umu ndi m’mene Paulo amakhalira kudzionetsera yekha pamaso pa Ambuye.

2. Kudzipereka kosankhidwa kudzera mu chikondi

Utumiki wa Paulo umationetsera za udindo wa kapolo weniweni omwe uli mu Chipangano Chakale. Ngakhale atapatsidwa mpata opita ngati mfulu, kapolo amatha kusankha kupitilirabe kukhala pansi pa mbuye wake chifukwa cha ubwino omwe unali pa mbuyeyo. Kwa Paulo, kukhala kapolo sichinali kuchepysedwa, koma iye amadziona  ngati ulemerero waukulu, osati ngati wantchito koma kukonderedwa, osati ngati moumilidzidwa koma ngati chisankho chake mu chikondi mwakufuna kwa iye mwini anadzipereka kwatunthu kwa Ambuye yemwe anamupulumutsa iye kuchokera ku tchimo ndi imfa.

3. Moyo okhadzikika pa chisomo
Kwa Paulo, utumuki wake ndi mphatso zonse, sanadziwerengere kapena kudzitenga kukhala chodziyeneredzera, koma amawerengera chisomo. Monga mwakubvomeledza  kwache, “mwa chisomo cha Mulungu  ine ndili chimene ndili” kuonetsera kuti, kukumana kwake ndi Ambuye pa nseu wa ku Damasiko, chinamukhadzikitsa kukhala odzichepetsa moyo wake onse. Ngati utumwi uli chabe kuyerekedza ndi wantchito, ndiye kuti, tili pansi pa watchitoyo. Maitanidwe, cholinga, komanso moyo wa mtumiki okhulupilira – zonse izi zinapatsidwa ndi Mulungu – zopanda pake koma mwa chisomo. Choona chake ndi choti Yesu Kristu ndi Ambuye wathu ndi chimwemwe chathu cha muyaya. Tiyeni tidzindikire choonadi cha uzimu ichi. Tiyeni tikhadzikitse malingiliro abwino pamaso pa Mulungu ndipo tiyeni ichi chikhale madziko a moyo watsopano.

Abusa Sung-Hyun Kim 

31 Ogasiti, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Kapolo wa Yesu Khristu
Aroma 1:1

Abusa Sung-Hyun Kim