Chipangano Chakale
(Aroma 1:2 )
“Khala-chete – Kodi si Afarisi ndi Alembi omwe ankadziwa bwino Chipangano Chakale? Ngati Chipangano Chakale chimanena za Uthenga Wabwino, ndi chifukwa chiyani sanamuvomeledze Yesu? Ndi chifukwa chiyani kuti mpaka anakana Uthenga Wabwino? Kodi izi ndi chifukwa choti Chipangano Chakale sichinalumikidzidwe bwino ndi Uthenga Wabwinowu?
1. Kukhala Muchiyanjano Ndi Mulungu
Afarisi ndi Alembi sadakhadzikike kwambiri moona M’malembo Oyera, koma mu chikhalidwe cha Aphunzitsi a Chilamulo. Ambuye anawadzudzula za ichi, nachitchula kuti, “chipembedzo cha anthu” izi sizinachokera kwa Mulungu ayi. Koma m’chitidwe wa otsogolera omwe amakhadzikitsa motsogozedwa ndi zokhumba zawo, monga atsogoleri a chipembedzo pamene akutsogolera anthu. Ngakhale kuti chimavekedwa maonekedwe a Mau a Mulungu, chimasoweka chinthu chomwe chili chofunika kwambiri – kukhala muchiyanjano ndi Mulungu
2. Nkhalapakati wa Uthenga Wabwino
Kukanakhala kuti Afarisi ndi Alembi analemekedza Malemba Oyera moona mtima, akanakhala ndithu ndi kuthekera komudzindikira Yesu. Chifukwa Malemba Oyera ananena mobweredzabweredza kudzera mu mauneneri osawerengeka za choonadi cha Uthenga Wabwino, komanso za momwe umo adzakhalira Iye yemwe ali Nkhalapakati wa Uthenga Wabwino. “Koma Iye analasidwa cifukwa ca zolakwa zathu, natundudzidwa cifukwa ca mphulupulu zathu, cilango cotitengera ife mtendere cinamgwera Iye, ndipo ndi mikwingwirima yace ife taciritsidwa.” (YESAYA 53:5) Zodziwika bwino ndithu, Izi sizinalembedwe ndi ophunzira a Yesu, koma n’neneri Yesaya, mu dzaka madzana asanu ndi awiri, Iye asanabwere.
3. Uthenga Wabwino unalonjezedwa nthawi za m’mbuyo
Paulo amatsutsidwa motere, “Munthu uyu akunena motsutsana ndi Mose ndipo kuphunzitsa zinthu zimene sizili mu Malemba Oyera,” koma Paulo amanenetsa kuti Uthenga Wabwino unalonjedzedwa nthawi ya m’mbuyo, M’malemba Oyera kudzera kwa aneneri. Uwu ndi Uthenga Wabwino omwe tsopano wapatsidwa kwa ife, kwa iwo omwe dziko lapansi silinawawerengera ngati kanthu, Mulungu anakhala chete munthawi yaitali mbuyomu kufikira nthawi imene anapereka Uthenga Wabwinowu. Mosawerengera kuti dziko lapasi litinyengerera ndi zokoma zake zili m’menemo, komanso mosawerengera kuti libweretsa zovuta ndi zowawa za mtundu wanji – Tiyeni tisatembenukire kutsutsana ndi Uthenga Wabwino. Tiyeni tikhadzikikemo mpaka chimalidziro ndi kulandira Mtendere wosatha wa Mulungu.
Abusa Sung-Hyun Kim
Septemba 14, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Uthenga Wabwino Wopatsidwa Mu Malemba Apaulendo
Aroma 1:2
Abusa Sung-Hyun Kim


