Mphamvu Ya Kuuka Ku Imfa

(Aroma 1:3-4)


“Chikondi cha Mulungu? Zoonadi, Mulungu sindimudziwitsitsa chifukwa ali Kumwamba komwe kuli kutali kwambiri, ine ndili pansi pano kutsautsika ndi moyo tsiku ndi tsiku. Koma Iye akudziwa zowawa zomwe ine ndikudutsamo? Chabwino ngati amadziwa, Kodi Iye akusamala za izi?”

1. Za Umwana
Anthu ambiri amaligalira motere – Koma pali choonadi chenicheni chomwe chimachotsa kukaikira kotere. Mwana wa Mulungu anasiya zonse, ulemerero onse omwe anali nao ndi kukodwera kosatha, ndipo anakhala monga mwa thupi. Kuti Mulungu asandulike mwa thupi kwa thunthu, kusintha kosasinthika. Mumanena kuti chikondi cha Mulungu ndi chosaoneka? Sichoncho. Chifukwa cha chikondi ichi, Mulungu anabwera mwa Iye yekha pansi pano pamene ife tili lero.

2. Chisoni
Ndi chifukwa ciani Iye yemwe anali ofanana ndi Mulungu anabwera ku dziko lino lapansi? Iye anadzikanidza yekha zonse zamphamvu ndi ulemerero wamuyaya mwa Umulungu onse, ndipo anadzichepetsa yekha kufikira pa Umwana, ndi kumvera konse komwe kunamutengera kumufikitsa ku imfa. Iye anathedwa mphamvu, anamva njala, ndi zowawa zonse monga umo zikhalira ndi ife. Anaona zisoni, zolemetsa , ndi zokhumudwitsa za moyo uno – ndi zambiri zomwe tikukumana nazo mu ulendo wa moyo – ndipo Iye anadziwa kuwawa ndi kupweteka mu moyo wa thupi mosawerengera za chisomo cha Mulungu chomwe chinali pa iye. Kodi tikhalabe okaikira za Mulungu amaneyu? Iye amadziwa za moyo wathu mwakuya kwambiri kuposa umo tidzidziwira ife eni.

3. Zotsimikidzira
“Ndikhulupilira bwanji kuti izi ndi zoona?” Ndi funso labwino ndithu. Koma pali umboni otsimikidzika, wa kuuka ku imfa. Mphamvu ya kugonjetsa imfa ili mwa Mulungu yekha basi. Ngakhale anthu anamukhomera Yesu pa mtanda ndi kumupha. Iye anauuka ku imfa tsiku lachitatu. Ichi chinachotsa kukaikira konse – muchoonadi chonse iye ali Mwana wa Mulungu. Iye amane achotsa machimo athu ndi kutipatsa ife moyo wosatha – kuuka ku imfa ndiko kutsimikidzira  ndi kulengedzetsa  komalidza kuti Yesu Kristu ndi Mulungu.

Septemba 28, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Mwana wa Mulungu wokhala ndi mphamvu ya Kuuka
Aroma 1:3-4
Abusa Sung-Hyun Kim