Mphamvu Ya Uthenga Wabwino
(Aroma 1:16-17)
Paulo sanasiye kulalikira Uthenga Wabwino, ngakhale amakumana ndi zovuta ndi zowawa konse komwe anali kupita. Ankachita izi chifukwa ankadziwa zazikulu za mphamvu zomwe Uthenga Wabwino umabweretsa.
1. Mphamvu Yaikulu
Mulungu ndi wamphamvu zonse. Palibe chamoyo pa dziko lapansi chomwe chingakwanitse kuima motsutsana ndi mphamvu yake. ndi yaikulu kwambiri, yowopsya, kotero kuti ilibe muyeso, ngakhale kufananizidwa . Zoonadi, Palibe chinthu chomwe mphamvu ya Mulungu singakwanilitse. Koposa zonse mu ntchito yonse, mphamvu yake yaikulu kwambiri ndiyo – mphamvu yomwe imabweretsa chipulumutso kwa aliyense yemwe wakhulupilira – mphamvu yakupulumutsa moyo wa munthu ku tchimo ndi chilango. Mphamvu iyi imapedzeka mu Uthenga Wabwino.
2. Uthenga Wabwino
Anthu amalemedwa kapena kuphinjika ndi Uthenga Wabwino, chifukwa amayankhula zinthu zosiyana ndi zomwe mitima yao ikukhumba, ichi chimakhala chinthu chomvetsa chisoni kuti ngakhale eni ake sadziwa chomwe ali. Mapeto ake, omwe akulalikira Uthenga Wabwino amaopa kuti anthu ena awasala ku magao ena komanso ubale wa pakati pao usokonekera. Ndi mtima oopa kukhumudwitsana, amayamba kulalikira Uthenga Wabwino koma mu njira yoti umveke mosangalatsa kwa anthu. Kodi Uthenga Wabwino omwe wabisa mtanda wa Yesu Kristu – Uthenga Wabwino omwe wapangidwa kukhala chokoma pakati pa anthu osakhulupilira – ukuyenera mu choonadi chonse kutchedwa Uthenga Wabwino? Kodi mphamvu ya Mulungu, yakupulumutsa miyoyo kunsinga zomangidwa ndi Mdierekezi nkotheka kubvumbulutsidwa kudzera mu Uthenga Wabwino onga uwu?
3. Udindo Wathu
Ngakhale anthu a dziko lapansi pano amatenga Uthenga Wabwino ngati chopusa, ngati mwala opunthwitsa, Koma ife omwe tinapulumutsidwa, sitiyenera kuchita manyazi ndi Uthenga Wabwino. Palibe mphamvu ku dziko lapansi yomwe itha kupulumutsa munthu ku imfa ndi chionongeko, ku themberero ndi gehena. Koma kudzera mu mphamvu ya Mulungu timapangidwa kukhala amfulu ku mantha. Tsopano tiyenera kugwira ntchito ndi Mulungu ya kupulumutsa miyoyo. Izi ndi zosatheka kukwanilitsa pamene tigwira ntchito mwa mphamvu yathupi. Koma pokhapokha ngati Mulungu mwakufuna kwake agwira ntchito m’munda nzotheka kukwanilitsidwa. Kudzera mu Uthenga Wabwino kumulola Mulungu kugwira ntchito – uwu ndiye udindo wathu.
Novembala 9, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Mkwiyo wa Mulungu
Aroma 1:18
Abusa Sung-Hyun Kim



