Tchimo Lolimbana Ndi Choonadi
(Aroma 1:18-19)
Pamene anthu achita zomwe Mulungu adana nazo, mwa chisankho cha mitima yao mkwiyo wake umawagwera. Mkwiyo wa Mulungu umagwa pa munthu wina aliyense – okhulupilira kapena osakhulupilira mofanana – ndipo ichi chimaonesera chisapembedzo ndi chosalungama cha anthu.
1. Chisapembedzo ndi Chosalungama
Chisapembedzo zitanthauza za ubale wathu ndi Mulungu – izi zinena za makhalidwe oipa a anthu pamaso pa Mulungu. Kwa iwo omwe aima pansi pa Mulunngu, koma ali olambira monyenga mkwiyo uwu uli pa iwo. Chosalungama zitanthauza za ubale wa munthu ndi nzake – kuchita zinthu mozembaitsa kapena zopunthwitsa ena ndi kufuna kukwanilitsa zokhumba zako. Munthu ochita izi, sakhala pa ubale wabwino ndi Mulungu, chifukwa chisapembedzo ndi chosalungama nthawi zonse ndi zolumikidzana.
2. Ndi chifukwa ciani anthu satuluka mu tchimo
Omwe ali mu chisapembedzo ndi chisalungamo ndi anthu omwe aponderedza choonadi, machitidwe awo amaonetsera kukhumbitsa kolimbana komanso kutsutsa choonadi. Mulungu amanyatsidwa ndi tchimo loponderedza choonadi, kotero – “Ndichifukwa ciani anthu aumilira tchimo ili?” Chifukwa mkati mwa mitima yao amalingalira ichi ngati chinthu chopepuka kapena chaching’ono. namanena “Sikudzakhala mkwiyo wa Mulungu zonse zizatha basi” Izi ndi zoona ndithu osati kwa osakhulupilira okha komanso ngakhale okhulupilira. Kaya ndi okhulupilira kapena osakhulupilira koma yense oponderedza chilungamo sadzapulumuka ku mkwiyo wa Mulungu.
3. Udindo Wathu
Ena amasinkhasinkha kuti osakhulupilira, ndani yemwe sadziwa choonadi, amalingalira molakwika. Koma Mulungu amaika mwa iwo chinachake chowatengera iwo kumudziwa Iye. Ndi anthu okhawo omwe amasatira zokhumba za matupi awo. Motero adzaweruzidwa monga mwa kutsutsana kwao ndi choonadi. Okhulupilira ayenera kukhala osamalitsa kwambiri. Tisakhale ngati iwo amene mwakusadziwa amatsutsana ndi choonadi. Tiyeni timvetsetse za udindo omwe ife tilinao, kudzindikira chomwe tili lero, ndi kuphunzira za ulemelero wa Chisomo cha Mulungu. Ndipo tiyeni tiyende mu moyo owonetsera za ulemelero wa Chisomo.
Novembala 16, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Mkwiyo wa Mulungu pa kusalungama
Aroma 1:18-19
Abusa Sung-Hyun Kim


