Kusiyidwa
(Aroma 1:24-25)
Mulungu sagwilidzitsa kolimba anthu omwe akhadzikika mu choipa kulephera kuvomeledza ntchito zao zoipa. Machitidwe Ake pa anthu otere amakhala osakhadzikika ndipo amawapereka kukhala pansi pa mphamvu ya tchimo.
1. Ichi Sichabwino Konse
“Kumusiya winawake” Ichi chimaonetsera zowawitsa ndi moyo ophinjika pamene Mulungu wachotsa mkono Wake wa chitetedzo ndi ogwilidzitsa, munthu amasiyidwa kuti akhale oyenda mosogozedwa ndi tchimo popanda chomutetedzera, ndi liwiro lalikulu kumufikitsa ku chiwerudzo. Nthawi zonse malingaliro ake amakhadzikika m’chikodwerero cha zoipa, kotero nkosatheka kumubwenza. Machitidwe onyenga, mobweredzabweredza, izi zimabweretsa malire a ufulu pa moyo wake. Chifukwa chilango sichiperekedwa panthawi yomweyi, munthu otere amazinamidza mumtima “ndi kuti zonse zili bwino” koma chonsecho ali munyengo yoyenera chilango chochititsa mantha.
2. Tiyenera Kulira
Mtima wathu umasatira zilakolako zokhumba za thupi, koma tinaitanidwa kuti tilamulire izo. Pamene zilakolako zokhumba za thupi zioneseredwa kudzera m’matupi anthu, chonyansa chioneseredwanso ndipo ichi timachitchula kuti tchimo. Tchimo limanyazitsa ulemelero wa pa munthu ndi kuchotsa ulemu. Chosamvesetseka, m’malo molira chifukwa cha uchimo omwe waima, anthu amakhala ndi mantha polingalira za chobwera chotsatira pa kugwako. M’moyo wamakono anthu amayesera kugwirizitsa ungwiro mwa thupi, koma mbali ina akudzikanidza ku choonadi chomwe chimapulumutsa ndi kutetedza. mapeto ake zimachotsa ulemerero wa umunthu.
3. Tiyenera Kulapa
Machitidwe a Mulungu pa kulekerera kwa ochimwa, nthawi zambiri, sakhala ndi cholinga chowataya kwatunthu ayi. Ngakhale pali kusiyidwa kotero, Mulungu amayembekedzera kuti anthuo alape. Munthu anabwera kuno ku dziko lapansi kuti alape – ndipo kutheka uwu ndi mpata omalidza, koma kwa awo omwe akhadzikitsa mitima kukana kulapa, Mulungu amawasiya kuti apange chisankho chomalidza, kuli kwa iwo eni kusankha Mulungu kapena nyanja yamoto. Kotero, tiyeni tisalamuliridwe ndi zilakolako zokhumba za m’mitima, koma tisatire choonadi cha Mulungu, tiyeni tikumbukire chisomo chake ndipo tipite chitsogolo mu njira yomwe Iye ali kutitsogolera.
Abusa Sung – Hyun Kim
Zitunda 21, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Kusiyidwa ndi Mulungu
Aroma 1:24-25
Abusa Sung-Hyun Kim


