Nzeru ya Sayansi Yonyozitsa Mulungu

(Aroma 1:28-32)


Umunthu wachotsa choona chomwe Mulungu ali kudzera mu chidziwitso cha sayansi. Kutengera mu chidziwitso chawo anamuyesa ndipo anamukana Iye kumutenga “wosayenera”  – osati monga wolengedwa – omwe tiyenera kuyesedwa ndi Mulungu – koma tayesera kumuyesa Iye, komanso mwadala amukana Iye mu miyoyo yawo.

1. Kugwa Kosankha Mwadala
Pamene anthu anamunyodza Mulungu,  kowirikidza anawapereka ku mtima wokanika. Anawaleka iwo kuti achite monga akhumba mwa zofuna zao – zakukana Mulungu , koma adzakomana ndi zovuta zenizeni. Palibe chifukwa chomufikitsa munthu kukhala kakasi monga ichi, Komabe, Mulungu safuna kuti munthu atayike. Amafunitsitsa kuti munthu adzindikire kuti ali kakasi ndipo ali osiyidwa mwa ichi ayenera kubwerera ku kulapa.

2. Kuonongedwa Kwa Khalidwe

Anthu anaperekedwa ndi kupasidwa mtima opanga choipa chonse, komanso kutenga ichi ngati chopereka mtendere mkati mwao. Amachita zinthu mwa dumbo ndi kaduka, sakondwera pamene ena achita bwino, amakonda ndeu, izi amachita nthawi zina mozembaisa komanso nthawi zina moonesera, amapunthwitsa ena mopanda manyazi. Akumuda Mulungu, amakhala osangalala pamene ena ali pamavuto, amadzitukumula, ndipo nthawi zambiri sasunga mapangano, amatukutuku, nthawi zonse akhumba zinthu zoipa, amatsutsana ndi ulamuliro, alibe mtima omvetsera ena, komanso mitima yawo sisunga malonjedzo awo. Anthu sakhadzikika pa chifundo cha umunthu pamene akumana ndi anthu otere.

3. Gulu La Anthu Wolimbikitsa Choipa
Choipa ichi sichinakhadzikike pa anthu ochepa chabe, koma kuti ambiri abwera pamodzi molimba ngati mdima wa bii – iwo omwe apanga choipa – amalimbikitsa ena ambiri kuchita momwemonso, kotero choipa chimafalikira kwambiri, ndi kuima molimba kudzera mwa iwo. Amayetsera kuonesera chilungamo cha mwaiwo okha, koma pa choonadi, ali ngati amithenga a m’dierekezi, kupititsa patsogolo choipa pa dziko lapansi. Ife omwe tafikitsidwa ku moyo kudzera pa msembe ya Kristu, tisadzikhadzikitsire mwa ife chidziwitso cha dziko lapansi. Tiyenera kulemekedza Mulungu monga Oyamba ndi Otsiridza, pa cholinga chogwilidzitsa miyoyo kudzera mu kulapa kosalekedza. Tiyenera kuika Mulungu kukhala pakati pa mitima yathu.

Abusa Sung – Hyun Kim

Januwale 4, 2026 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Kuwapereka Kuti Akhale ndi Maganizo Otayika
Aroma 1:28-32
Abusa Sung-Hyun Kim