Kubwezera kwa Mulungu
(Aroma 2:8-10)
Mulungu amaungudza, kukumbukira komanso kulemba ntchito za munthu wina aliyense kudikilira chiwerudzo chomalidza. Chiwerudzo chidzafika pa wina aliyense popanda ngakhale m’modzi kupatulidwapo komanso mopanda kuchotsera chidzaperekedwa molingana ndi udindo wa munthu aliyense. Paulo akunenetsa, “Koma kwa iwo ofuna zaiwo okha ndi kusamvera choonadi, koma kumvera chosalungama – kuzaza ndi mkwiyo (AROMA 2:8) zizawagwera – chifukwa cha zokhumba zathu kuti tipedze chitonthozo pa zokhumba zamatupi omwe ife tili.
1. Okhumba Za Mitima Yao
Kusonkhana pa malo amodzi sitchimo, ichi chisiyana ndi pamene wina atseka maso ku choonadi ndi kuwabweretsa anthu malo amodzi ndi mtima olunjika pa zokhumba zao. Kugwededza dera ndi mbiri yabodza ndi kuonetsera mphamvu zoipa. “Tchimo lofuna za iwo okha” Ichi sichionetseredwa ndi machitedwe akuthupi oneka ndi maso, koma kuchokera ku mtima wachinyengo omwe utsutsa choonadi ndi kugwilitsa ntchito chosalungama ngati njira yokwanilitsa zokhumba zao.
2. Otsatira Chosalungama
Palibe amene amabvomeledza poyera kuti, “Ndimatsutsana ndi choonadi” Chonsecho, onse okana choonadi amakhala mosogozedwa ndi zokonda ndi njira za dziko lapansi. Chifukwa palibe mbali ya chikatikati mu dziko la uzimu, moyo uwu pang’ono ndi pang’ono umalunjika ku chosalungama. Maonekedwe alero a iwo otsutsana ndi Abusa awo ndi kusolola malupanga kilimbana ndi Tchalichi uku ndi kubvumbulutsidwa kwa chitsogodzo chakugwa.
3. Omwe Achita Zabwino
“Mazunzo ndi zowawa ” zaperekedwa kwa omwe akusatira chosalungama, pamene ulemerero, ulemu ndi mtendere zaperekedwa kwa amene achita zabwino monga mwa choonadi. Ngakhale okhulupilira sangathe kuchita zabwino mukuthekera kwa paiwo okha. Monga m’mene chiliri chipulumutso chopatsidwa mwachisomo, moyo wachiyero umakhadzikika kudzera mu mphamvu ya Mzimu Woyere yekha. Kwa iwo omwe anataya mtima omanga zokomera iwo okha m’malo mwake afunafuna mphamvu kuti akondweretse Ambuye. Mulungu mwachidziwikire azawabwezera ulemelero, ulemu ndi mtendere.
Abusa Sung – Hyun Kim
Febuluwale 22, 2026 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Wochita Zoipa ndi Wogwira Ntchito Zabwino
Aroma 2:8-10
Abusa Sung-Hyun Kim



