Chiwerudzo Chopanda Kukondera
(Aroma 2:11-12)
Ku dziko lapansi, timawerudza anthu mwamaonekedwe akuthupi, ichi chili chinthu chodziwika bwino. Momwemonso achitira ngakhale ku mabwalo amalamulo. kumene kukondera chili chinthu chopereka chiopysezo. Koma chiwerudzo cha Mulungu chili champhumphu chosakondera. Kusakondera kwake ndi kopambana kotero kuti amaonetsetsa kuti achite mwapadera kwa munthu aliyense monga umo waimira mumoyo wauzimu.
1. Zina Mwa Dongosolo Lake
Amitundu alibe chilamulo, komabe sanaikidwe kumbali pa kuima pa chiwerudzo. Mitima yao, chikumbumtima chawo komanso bvumbulutso la chilengedwe limawapatsa chidziwitso cha umulungu wa Mulungu. Adzawerudzidwa molingana ndi muyeso wa chidziwitso chomwe analandira. Ayuda adzawerudzidwa ndi chilamulo. Chifukwa kwa iwo analandira zambiri, undindo waonso ndi waukulu. “Nanga ndikotani kwa akristu omwe analandira Uthenga Wabwino?” Undindo waukulu kwambiri ukuyembekedzeredwa pa iwo.
2. Chisomo Chosatengera Ntchito
“24. Komanso ndinena kwa inu kuti dzuwa la kuweruza, mlandu wace wa Sodomu udzacepa ndi wako.” (MATEYU 11:24) Uyu ndi Yesu kupereka chenjedzo ku Kapernao. Anali ndi kukonderedwa kokumana ndi mwana wa Mulungu maso ndi maso, koma anamukana Iye. Machitidwe otsamwitsa onga awa akuonetseranso mwa anthu omwe anadziwa chilungamo cha Mulungu koma anasankha kuchipatukira mwadala. Buku la AHEBRI likupereka chenjedzo lolamitsa; Nkosatheka kwa munthu yemwe anagwa atalawa mphamvu ya nyengo ilimkudza kuti akonzedwenso kachiwiri kuti afikire ku kulapa. (AHEBRI 6:4-6)
3. Chiyembekedzo Chokhacho
Nkosatheka kupulumuka ku chiwerudzo chopanda kukondera cha Mulunngu mwa ife tokha. Chifukwa cha ichi tiyenera kudalira pa Yesu Kristu. Tayenera kulandira chionongeko chifukwa cha machimo athu. Koma talandira chikondi cha Mulungu. Yesu Kristu ali mphatso yamtemgo wache ya Mulungu ndi chiyembekedzo chokhacho. Sitikuyenera kumulola kuti achoke ku mbali yathu. Tiyeni tsopano tilape ndi mtima onse ndi kubwerera kwa Iye. Tiyeni molimbika tiyambe kukhala moyo ngati omwe akhalira odzutsidwanso.
Abusa Sung – Hyun Kim
Lachiwiri 1, 2026 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Chiwerudzo Chopanda Kukondera
Aroma 2:11-12
Abusa Sung-Hyun Kim


