Akulu Pansi pa Ambuye
(Aefeso 6:9)
Dziko lapansi nthawi zonse limatiumiliza kukhala anthu opikisana, kudandaulana, komanso kumenyana. Koma akristu amakhala mu chidziwitso cha Ambuye ali m,Mwamba. Kukhulupilira mwa Mulungu olungama yemwe adzawerudza zinthu zonse mwachilungamo, amakhala okhulupirika ku udindo omwe apatsidwa lero, komanso kuonetsera chilungamo cha Mulungu amene ali mwa iwo.
1. Ubale odzipereka kwa tunthu kwa wina ndi nzake
“Mtumiki osakhulupirika – akulu oipa” Maganizo awa ndi okhadzikika pa dziko lapansi, koma choonadi chake, kaya wina ndi otumikira kapena wankulu, koma onse ali ndi mbali yokhala adindo. Akulu sayenera kugwiritsa ntchito udindo wao molakwika, koma kuti kukhala munthu osenza udindo m’malo mwa anthu ena. Ubale wabwino wa pakati pa otumikira ndi ambuye awo umakhazikika pamene pali kudzipereka kwenikweni kwa wina ndi nzake. Akulu ayenera kuonesesa kuti anthu omwe akuwatsogolera ndi okondwera, ndipo otumikira ayenera kuikapo mtima kumvetsetsa zokhumba za ambuye awo.
2. Omwe atumikira Ambuye m’modzi
M’mene zilili kuti otumikira amvera ambuye awo mwa Kristu, momwemonso akulu awo ayenera kuchitira izi anthu omwe akuwatumikira. Izi zili motero chifukwa akulu ndi owatumikira onse ali pansi pa Ambuye m’modzi. Makhalidwe ndi machitidwe omwe akulu achitira owatumikira, atsimikidzira chimodzimodzi ndi m’mene achitira ndi Ambuye wao omwe ali m,Mwamba. Ngati akulu satha kupewa m’kwiyo, komanso kuchitira zoipa owatumikira, izi zimapangitsa kuti kukhale kovuta kuti owatumikira awamvere, komanso kutaya chidwi chogwira ntchito zao mokhulupirika, akulu asaiwale kuti ali ndi ulamuliro omwe uli ochitachita komanso wapakanthawi, osati wamuyaya.
3. Ambuye oweruza mwa chilungamo
Dziko lapansi, mwa chidzolowezi ndi mwa chikhalidwe limakhulupilira kuti anthu omwe ali ndi maudindo amaonera pansi anthu omwe ali pansi pao, Komanso kuchita zinthu moonetsera mphamvu zao. Koma Mulungu alibe tsankhu pakati pa anthu. Ndizotheka kuti udindo omwe ali nao ku dziko lapansi suzalingana ndi chomwe adzakhale pa tsiku la chiweruzo. Mosawerengera ndi nyengo zomwe munthu akudutsa, aliyense adzaweruzidwa monga mwa ntchito zake. Kwa wina aliyense ochita zoipa, kudzakhala masautso akulu ndi zowawa, koma kwa onse ochita zabwino, kudzakhala ulemerero, kulemekedzedwa ndi mtendere.
Abusa Sung-Hyun Kim
1 Juni, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Akulu Achikristu Omwe Amatumikira Antchito Awo
Aefeso 6:9
Abusa Sung-Hyun Kim