Awo omwe ali oitanidwa

(Aroma 1:7)


Maitanidwe a Mulungu sali monga mwa kukhumba kwa munthu mwa chisankho cha mtima wake. Amamangilirika ku ntchito yaikulu yokwedza dzina Lake, ndipo pa chifukwa ichi Mulungu amayang’anira maitanidwe Ake pa ife ngati chinthu chamtengo wake chofunika. Sawasiya konse onse aiwo omwe anaitanidwa mwa cholinga Chake.

1.  Omwe ali okondedwa Ake.
Mulungu anaitana ife chifukwa tili okondedwa Ake. Chikondi cha dziko lapansi nthawi zonse chimakhala ndi zokhumba zobisika, koma chikondi cha Mulungu sichili chomwechi. Ndi chikondi chomwe chamangilirika pa udindo komanso chotsimikidzira ndi ntchito. mosafanana ndi chikondi cha dziko la pansi. Ife sitinayenere kulandira chikondi chotere, koma kudzera mwa Kristu, Mulungu anatsegula njira kwa ife kuti tilandire ichi.

2. Omwe ali odzipatulira mwapadera kwa Mulungu.
Omwe amalandira chikondi chodabwitsa ndi maitanidwe a mtengo wapatali sakhala anthu opita ku Tchalichi mwachipembedzo – awa ndi oyeretsedwa – opatulidwa mwa Mulungu. “Oyera Mtima”  ndi dzina la ulemerero, makamaka okonzekeretsedwa kwa iwo amayenda mu ulemerero Wake. Mosawerengera zofooka zathu, kudzera mu maitanidwe talandira kukhala ansembe oyera mtima ndi kutengapo mbali mu ntchito yachipulumutso ya Mulungu. Maitanidwe awa sapatsidwa kwa ife chifukwa choti ife ndife oyenera ayi, koma kuti mwa chisomo basi.  Kotero – tiyeni tisadzikanidze ku izi chifukwa cha zofooka zathu – koma tibvomeredze chomwe ife tili – kwa iwo omwe apatulidwa akwedze dzina la Kristu.

3. Iwo omwe akhalabe okhulupirika.
Kwa iwo omwe ali okondedwa Ache a Mulungu ndipo anaitanidwa  kukhala oyera, Mulungu amawapatsa m’dalitso – chisomo ndi mtendere. Kudzera mu m’dalitso, timalilaka dziko lapansi – ndipo timaima molimba kupita chitsogolo mu chipambano chamuyaya. Nanga kodi mudakali otsinkhatsinka. “Ndi zoona Mulungu angaitane munthu onga ngati ine?” Chofunikira kwambiri m’mitima yanu – ndicho kukhumbitsa kukhulupilira mwa Yesu, za kulapa tchimo, ndi kukhadzikika mu kumvera Ambuye – ichi ndi chitsimikidzo choti Ambuye akugwira ntchito mwa iwe. Kuitana Kwake sichili chithu chopanda pake. Mosawerengera nyengo yomwe tikudutsamo – tiyeni tikhale okhulupirika ku ntchito yomwe Mulungu watiyitana ife, Ndife miyoyo yoyenera kukhala mwansangala kwambiri mwa onse a padziko lapansi, awa ndi iwo omwe Mulungu sadzawataya.

Okutobala 12, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Chigamulo popanda kusankha mbali
Aroma 1:5-7
Abusa Sung-Hyun Kim