Chinyengo Chachikulu
(Aroma 1:26-27)
Chinyengo chauzimu ndi chinyengo chakuthupi zili ngati mbali ziwiri za kobili lilodzi. Chinyengo chauzimu nthawi zonse chimayenda mosogozana ndi machitachita owonetsera chinyengocho muthupi. Ngati anthu apembedza zinthu zolengedwa m’malo mwa Mulungu ndi kumukana moumitsa mitima, Mulungu amawapereka mu changu chochititsa manyazi. Ichi Baibulo limatanthauzira ngati chamanyazi monga kukhalira pamodzi pa amuna okha okha monga umo achitira ndi nkazi ngati chitsanzo chabwino.
1. Iwo Ochita Motsutsana Ndi Chilengedwe
Kukhalira pamodzi kwa amuna okhaokha monga achitira ndi nkazi chimatengedwa ngati “kusintha machitidwe wogwilitsa tchito motsutsana ndi chilengedwe.” Pakumusiya Mulengi, izi zitsimikidzira kuonongedwa kwa dongosolo lomwe Iye anakhadzikitsa. Tikaona abambo a ku Sodomu , ngakhale kuti anakanthidwa ndi khungu m’maso ao ngati chilango chotsatira pamene amayesera kuchita motsutsana ndi ufulu wa alendo omwe anafika kwa Loti, anayesera kusaka khomo ngati zinzukwa mpaka anafika pothodwa. Zilakolako zoipa zathupi zimaipsya malingiliro ndi kuononga mitima yao monga moto owononga. Ngakhale dziko lapansi limadziyeneredza kudzilungamitsa ku ichi mu njira yao, Mulungu adana naza ndithu.
2. Palibe Dongosolo Losiyanitsa Anthu Munsinkhu Kapena Udindo Ku Mbali Ya Tchimo
Modziwika bwino, Baibulo silinena kuti kukhalira malo amodzi abambo okhaokha ngati umo achitira ndi nkazi ndi vuto lokhalo pakati pa anthu, pali kukhalira malo amodzi pakati pa anthu osakwatira, kuledzera, njiru, kudzikweza, komanso ena odzetsa chokhumudwitsa – palibe m’modzi mwa awa omwe adzalowa mu ufumu wa Mulungu. Choipa ichi chilinso pa anthu oyesera kuononga ndi kubweretsa mipatuko mu Mpingo mosawerengera kuti chisomo chinaperekedwa kwa iwo, onyenga olengedza mbiri yopotodza, ndi ena opotodza choonadi ali obweretsa chophyinja pa Mpingo. Ichi ndi chowawa kuposa m’chitidwe okhalira malo amodzi anthu amuna kapena akazi okhaokha. Palibe kulemekedzedwa kuti uyu ndi wamkulu, kapena kuti uyu ndi wa udindo wapamwamba pamene munthu wakodwa mu tchimo – pamene ena achita tchimo akhala chiipire, komanso ena amabvomeledza. Pokhapokha kuti walapa, koma onse adzawerudzidwa mofanana.
3. Kulapa Kokha Ndiye Yankho
M’chitidwe okhalira malo amodzi anthu ofanana chilengedwe ndikotheka kukhululukidwa ndithu – ngati alapa, monga umo munthu wochita katangale sabadwa ali wakatangale, tchimo silinaikidwiretu mwamunthu pachiyambi kuti lidzaonekere patsogolo. Ngati tadzipedza tokha kukhala ochita motsutsana ndi choonadi cha Mulungu, mosawerengera kuti ndi tchimo lotani, sitiyenera kupedza njira yodzitsimikidzira mwaife tokha podzipedzera njira zoziyeneredza ngati olungama koma modzichepetsa kubwera pa Mtanda. Mulungu kwakukulu amakhumbitsitsa kuti tisataike koma tikhale ndi moyo monga anthu oyera mtima mu choonadi.
Abusa Sung – Hyun Kim
Zitunda 28, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Kuwasiya m’Zilakolako Zonyansa
Aroma 1:26-27
Abusa Sung-Hyun Kim


