Chisoti cha Chipulumutso
(Aefeso 6:17)
Ngakhale pa nyanja ya dziko lapansi pauka mafunde wopsya – Akristu owerengeka amaima molimba – monga sitima imaima mozama – sisunthika kulunjika kwina. Amakumana ndi chiwerudzo chopanda chilungamo, amayetsedwa mu nyengo zoti tsogolo silioneka. Chonsecho mwadongosola labwino samagwa mu choipa.
1. Lupanga la n’dani limatema mutu
Ngakhale amaoneka osweka kunja – mkati mwa mitima yao mumakhala kutsimikidzika – “Ndipulumutsidwa ndithu.” Chifukwa cha kulimbika mtima uku, sagwededzeka. Ngakhale kuti msilikali atadzikolekera zovala zamphamvu motani – Koma ngati n’dani wake amumenya m’mutu ndi lupanga la mphamvu – amagwa nthawi yomweyo. Ichi ndi chifukwa chomwe msilikali aliyense popita ku nkhondo amabvala chisoti. Ichi chili chomwecho mu nkhondo ya uzimu.
2. Madziko a chiyembekedzo a chipulumutso
N’dani wathu amabaya mumalingiliro athu ndi maganizo onga awa, “Ine ndi zoona kuti ndinapulumutsidwadi?” Kapena, “Ndikwanitsadi kugwiritsitsa chipulumutso changa mpaka nthawi yomalidza?” Pamene talemedwa ndi zolemetsa za moyo uno – Kapena zotsamwitsa kudzera mumasautso, amaonjedzera kusolola lupanga lake mochititsa mantha kwambiri. Chimatitetedzera ife ku nkhondo yopsya ngati iyi ndi chisoti – madziko a chiyembekedzo a chipulumutso. Tsiku limene Ambuye adzabweranso, tidzaukitsidwa ku imfa ndipo pakutha pa zonse tidzakhala naye limodzi mu ulemerero wa Kumwamba.
3. Moyo odzipereka kwatunthu ku Uthenga Wabwino
Ambuye ananena Mau awa kuti tisataye mitima, “Mtendere ndikusiyirani – mtendere wanga ndikupatsani – ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa,” “Dziko lapansi mudzakumana ndi masautso, Koma khalani okondwera. Ine ndinalilaka dziko lapansi.” “Ichi ndi cholinga cha Atate yemwe anandituma Ine. Kuti Iye anapatsa zonse kwa Ine, kuti ndisatayepo chilichonse. Koma kuti ndikadzutse zonse mumatsiku omalidza.” Iwo omwe afunitsitsa kuima molimba mu chiyembekedzo cha chipulumutso ayenera kukhala ofunitsitsa kudzipereka kwatunthu okha ku Uthenga Wabwino. Nthawi zina amamva ngati asiyidwa, kusamvesesa – kapena kuiwala chifukwa cha kukumbukira zina – Koma Ambuye samawasiya onse omwe amamufunafuna Iye ndi kudalira Iye. Ndi mphamvu yake adzawasunga mpaka nthawi yomalidza ndi kutha kwa zonse – adzawaonetsera opanda banga mu ulemerero wa Mulungu.
Abusa Sung-Hyun Kim
27 Julayi, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Chisoti cha Chipulumutso
Aefeso 6:17
Abusa Sung-Hyun Kim


