Chiyembekezo Cha Kuuka Kwa Akufa
(1 Atesalonika 4:13-18)
Yesu anauka ku imfa chifukwa Mulungu Atate anamudzutsa. Ndi chifukwa ciani Mulungu anamudzutsa ku imfa? Chifukwa Mulungu anakodwera ndi nsembe yomwe Yesu anapereka. Kuuka ku imfa kwa Yesu ndi umboni oti Mulungu anamuvomeleza Iye.
1. Mphamvu ya imfa inathyoledwa
Mu kuuka ku imfa, Yesu anathyola mphamvu ya imfa. Tsopano, onse omwe ali mwa Iye sadutsa mu imfa yomwe Iye anadutsamo. Indee, onse omwe ali mwa Yesu amakhala ali a moyo ngakhale matupi awo a nyama atasiya kugwira ntchito. Kunena kuti, sikukhala kufa – koma kuti kumakhala kugona tulo kwa kanthawi.
2. Tsiku lomwe Ambuye adzabweranso
Onse omwe anagona tulo mwa Ambuye adzaukanso. Zidzachitika liti? Zidzachitika pamene Yesu adzabweranso. Pamene Ambuye adzatsika mlengalenga. Okhulupilira Ambuye omwe adzakhala ali a moyo adzakwatulidwa kupita mlengalenga kumene Ambuye ali. Nthawi iyi matupi awo sadzakhala opangidwa kuchokera ku fumbi, (dothi) adzasandulika matupi a ulemerero. Nanga kudzatani kwa iwo amene anagona tulo, awo – anafa mwa Yesu? Adzakomana ndi Ambuye atabvekedwa matupi a ulemerero, komanso ngakhale pakati pa oyera mtima omwe adazakhale adakali moyo ku dziko lapasnsi.
3. Njira yodzala ndi chiyembekezo
Ndi zotheka kuchoka ku dziko lapansi nthawi yomwe Ambuye adzakhala asanabwere kachiwiri, kapena tidzakhala tili moyo mpaka tsiku lomwe Iye adzabwera. Mulimonsemo, kwa iwo omwe alibe chiyembekezo cha kuuka kwa akufa, tsiku ili lidzakhala tsiku la tsoka. Koma kwa ife, siziri chomwecho. Ngakhale kuti kudzakhala kulira chifukwa chowawidwa mtima chifukwa choti tidzasiyanitsidwa ndi anthu owme ali okondedwa athu. Koma kulira kwake sikudzakhala kopanda chiyembekezo. Pamene Ambuye adzabweranso, onse omwe ali mwa Iye adzakomana nayenso. Chotero, tiyeni tiyende mu njira ya moyo monga umo Ambuye afunira, poika mitima yathu pa tsiku ili, ndi chiyembekzo chonse.
Abusa Sung-Hyun Kim
Epulo 13, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Chiyembekezo cha Mpingo pa Kuuka kwa Akufa
1 Atesalonika 4:13-18
Abusa Sung-Hyun Kim