Chodzimangirira Cha Choonadi
(Aefeso 6:13-14)
M’katikati mwa nyengo zolimba mu moyo wamunthu, anthu ena amayamba kufunsa mafunso onga awa,.”Ndichifukwa ciani Mulungu ali chete? Kodi Baibulo ndi choonadi chenicheni?” Kodi ndi zotheka kuti munthu yemwe akumukaikira Mulungu kumudalira Iye kwatunthu?
1. Kuthekera kokhala ndi chidziwitso cha zamutsogolo
Pamene munthu okhulupilira ayamba kukaikira Mulungu motere, zimatsimikidzira kuti machenjerero a mdierekezi pamoyo wake amugonjetsa. Okhulupilira ambiri amaika patsogolo chikhulupiriro kukhadzikika pa moyo ofuna kukhala mu zabwino zokhazokha nthawi zonse. Mumoyo wao salingilira za machenjedzo a nthawi zowawa, komanso sakhumbira kumva mau oti tiyenera kuima molimba kutsutsana ndi machenjerero a mdierekezi. Chonsecho izi ndi zimene mdierekezi amafunitsitsa nthawi zonse. Anthu otere nkosatheka kuima molimba motsutsana ndi machenjerero ake. Ndipo matsiridziro awo ndi odziwika bwino, mosakaika amachoka pa Uthenga wabwino, ndipo amaima modziyeneredza ngati okhulupilira, komanso mapeto a zonse amadzakhala chokhumudwitsa pa Mpingo chifukwa cha makhalidwe awo oipa.
2. Mtima Okhulupirika
Ichi ndi chifukwa chomwe tiyenera kuvala zida zonse za nkhondo ya Mulungu. Ndipo palibe mbali yoyamba yomwe tiyenera kutengapo kuposa kudzimangilira m’chuno mwathu ndi lamba wa choonadi. Izi ngati sizili m’malo mwake, palibe chilichonse chomwe chingatisatire. “Kudzimangirira m’chuno ndi lamba wa choonadi sizitanthuza kungodziwa kokha Mau achoonadi ayi, ‘Choonadi’ Chomwe tikuchinena pano ndiko kukhulupirika. Nthawi zina timanena kuti kukhala oona mtima, wagwiro, kapena kukhala wachilungamo mu Mau, ichi ndi chabwino ndithu.Choonadi chomwe Mulungu amayembekedzera pa ife ndicho kukhala okhulupirika mtima, ndi makhalidwe otiyenera abwino.
3. Chipatso cha Choonadi
Mwa ife tokha, nkosatheka kupedza kapena kukhala okhulupirika. Koma pokhapokha titaika mitima yathu kukhulupilira Mulungu, Mwaichi mu nyengo zonse timakhadzikika mu chiyembekedzo cha malonjedzano ake a kumwamba. Kubvomeredza m’mitima yathu kuti Mulungu ali nafe, komanso kumvera Mau Ake. Mulungu nthawi zonse amakwanilitsa chimene anachiyankhula. Onse omwe amakhulupilira Mulungu motero amakulirakulira m’chikhulupiliro. Amadzipereka kutumikira Mulungu mwa chiyembekedzo ndi mokondwera, ndipo pamene achita izi mowirikidza, mwa iwo chilungamo chimakulirakulira. Kotero tiyeni choyamba tidzimangirire lamba wa choonadi m’chuno mwathu ndi kusendera chifupi kwa Ambuye.
Abusa Sung-Hyun Kim
22 Juni, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Kumenyana motsutsana ndi Mphamvu Zazikulu Zokonzedwa za Mdani
Aefeso 6:12
Abusa Sung-Hyun Kim


