Chodzitetedzera cha Chikhulupiliro
(Aefeso 6:16)
“Kodi Mulungu wakhalandi M’dindo osunga moyo wanga mpaka nthawi yomalidza?” “Ndi Chifukwa ciani ali chikhalire chete osachitapo kanthu, mu nyengo yonga iyi?” Tsopano ndi kwabwino kuchita nao mwakuthekera kwanga.” Ngakhale kuti sitikhumbira izi, malingiliro otere amabwera mwa ife ndithu natisowetsa mtendere.
1. Mibvi yamoto.
Awa ndi machenjerero a uzimu a Mdierekezi. Amakhala tcheru kufufudza, kuonetsetsa zofooka za munthu aliyense ndi mosalekedza amaponya mibvi yosawerengeka. Mibvi yowopsya kwa iwo, cholinga chake sikubweretsa zokhumudwitsa kokha, koma kuti agwededzenso chikhulupiliro chathu pa Mulungu, mwachidziwikire amasokoneza ubale wa pakati pa Mpulumutsi ndi omwe Iye anawapulumutsa. “Ndi chifukwa ciani munthu okhulupilira amayamba kumukaikira Mulungu?Chifukwa Mdierekedzi amayesa ndi zinthu zooneka ngati thandizo kapena yankho – kudzera mu kukopa kwa mphamvu kotero – umu ndi m’mene achitira.”
2. Chodzitetedzera.
Pa nkhondo za masiku akale, mibvi yamoto inali zida zoopsya kwambiri. Simathera pamene yaboola ndi kulowa nthupi, imapitilira apa, imayatsa moto ndi kunyeketsa pamalo pomwe yabayapo. Ndipo malawi a moto amamwadzika ndi kuyatsa kalikonse koyandikira, ndipo kuononga chilichonse pamalopo. Tsopano talingalirani zinthu zochititsa mantha ngati izi, zikutsika ngati mvula kuchokera mlengalenga – pokhapokha asilikali akakhala ndi chodzitetedzera chachikulu – chopangidwa ndi thabwa lolimba kwambiri ndi chikopa cha mnofu waukulu, chonyikidwa m’madzi nkhondo isanayambe – sakanatha kutetedzedwa ku chiophyedzo chochititsa mantha ngati ichi.
3. Kukhulupilira.
Mulungu watipatsa ife chodzitetedzera monga ichi kwa iwo omwe ali pakati pa nkhondo ya uzimu. Ichi ndi, “chodzitetedzera cha chikhulupiliro,” Chikhulupiliro chomwe tikunena pano sichongokhulupilira dongosolo la chipembedzo kapena kudziwa mabvumbutso a zinsisi za Mau a Mulungu. Uku ndi kumukhulupilira Mulungu kwa tunthu ndi mtima onse monga munthu, kudalira kwatuthu mu malonjezano Ake, ndi Mau Ake, ndi zofuna zake, ndi dongoloso lake. Mulungu yemwe anatipulumutsa ife kudzera mwa Kristu, amene akutetedzera miyoyo yathu kufikira lero, ndipo adzatitetedzera ife kufikira tsiku lakuukitsidwa ku imfa – Iye salephera – kukhulupilira Mulungu uyu mpaka nthawi yomalidza – Ichi ndi chodzitetedzera chomwe chingadzime mibvi yonse yamoto ya Mdierekedzi.
Abusa Sung-Hyun Kim
20 Julayi, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Chodzitetedzera cha Chikhulupiliro
Aefeso 6:16
Abusa Sung-Hyun Kim


