Inu Omwe Muweruza Ena

(Aroma 2:1)


Kwa a Yuda omwe amadziona olungama ndi kuweruza machitidwe a anthu Amitundu, Mtumwi Paulo akuti. “Cifukwa cace uli wopanda mau owiringula, munthu iwe, amene uli yense wakuweruza umacita zomwezo.”

1. Mumadziwa Chabwino
Pakuona umo a Yuda achitira powerudza Amitundu zitsimikidzira kuti anadziwa kale choonadi chomwe chili chabwino ndi choipa pamaso pa Mulungu, pamene Amitundu amadzindikira chabwino ku choipa kudzera mwakuwungudza mwa chikumbumtima ndipo kwa a Yuda kunapatsidwa chowonjedzera ndicho bvumbulutso la Mulungu. Ngati anthu awa apitiliza kuchita tchimo pamaso pa Mulungu, kodi sadzalandira chilango chachikulu kuposa Amitudu omwe sanalandire bvumbulutso? Ichi chili chimodzimodzi kwa ife, monga akristu, tiyenera kukumbukira kuti pamene tikudzitukumula kwakukulu pa chidziwitso cha choonadi cha anthu tiyembekedzere kudzakhala ndi udindo waukulu pantchito zathu patsogolo.

2. Kuziyeneredza Kosatha Kwa Anthu
Ambuye anati watchito yemwe adziwa zokhumba za mbuye wake koma asankha kuchita mosayenera adzalangidwa kwambiri (Luka 12:47) . Anthu amaweruza ena ndi nzeru za umunthu, chonsecho iwo ali odzikudza koposa mwa iwo okha. Amalodza kachitsotso m’maso mwa ena, koma kulephera kudzindikira mtanda omwe uli m’maso mwao. Ambuye akuchenjedza omwe amapeputsa chilungamo cha Mulungu ndi muyeso wa ntchimo lao. “Ndi muyeso omwe tiyesera ena – omweo tidzayesedwa nao” (Mateyu 7:2)

3. Nkosatheka Kudzizindikira Wekha Chomwe Uli
Palibe uyo atha kuweruza wina – chifukwa tonse tili osalungama. Wina kufunsa kuti, “Koma ine sindinachitepo chosalungama?” Ambuye akuyankha, “Ngati mtima wako uli odetsedwa ndi choipa, ndiye kuti uli ochimwa ndithu, chomwe tikusowekera ndi kulapa. Ichi ndi choonadi kwa omwe akudziwa bwino za Mulungu. Tiyeni tisanyalapsye mphamvu ya tchimo. Tisakhalenso akuweruza ena. M’malo mwake, tiyeni tiyang’anire za choonadi cha ife tokha, tifunefune chikhululukiro cha Mulungu ku nthawi zonse za moyo wathu ndi kupitilira kugonjetsa zofooka zathu podalira mphamvu ya Mzimu Woyera.

Abusa Sung – Hyun Kim

Januwale 11, 2026 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Inu Omwe Muweruza Ena
Aroma 2:1
Abusa Sung-Hyun Kim