Kokonda Ngati Kristu

(Aefeso 5:25)


“Mkazi wanga sandilemekeza, Ine ndimukonderanji? Ngati sindikuchimva mu mtima mwanga, Ndiziumiriziranji kutero? ” Inde, ukungoyenera kutero. Zoonadi chifukwa ndi chomveka bwino. Sizitengera kuti nzangoyu ngotani, Chifukwa choti uli mwa Kristu, Ichi ndi chifukwa chokwana.

1. Pamene pali chosowa
Ndi chifukwa chiyani Samariya anathandiza Myuda pamene anali pang’ono kufa pomwe anavulazidwa ndi achiwembu? Kapena chifukwa anali ndi chuma chambiri? Kapena anali okondeka? Ayi, sizinali chomwecho. Panali chifukwa chimodzi – Chifukwa anali kusowa thandizo. Chimodzimodzi ndi chikondi cha Kristu kwa ife. Amatikonda osati chifukwa ndife okondedwa ake, koma chifukwa popanda chikondi chake sitingakhale ndi moyo.

2. Chisankho chokonda ndi mtima onse
Chikondi cha mwamuna kwa mkazi wake chiyenera kukhalanso motero. Amamukondabe mkazi wake ngakhale makhalidwe ake ali osamuyenereza kutero, koma kuti mkaziyo amasowa chikondi cha mwamuna wake. Chikondi sichitengera makhalidwe – koma ndi chisanko. Monga Ambuye anasambitsa mapazi a ophunzira ache, ngakhale amadziwa mwano ndi kusakhulupirika kwao – koma anasankha kuwakondabe. Sichisankho cha ka phindi, koma izi ndi zoyenera kuchita tsiku ndi tsiku. Ndi chifukwa chake chikondi chapatsidwa kapena kulamuliridwa ngati lamulo.

3. Chikondi chimaoneseredwa kudzera mu kupereka
Chikondi cha dziko lapansi chili ndi zokhumba zake. koma chikondi cha Mulungu umadzipereka kuchokera pansi pa mtima. Ngakhale asanafike ku dziko lapansi Yesu Kristu anadziwa kale zowawa ndi zokhoma zomwe zimamudikirira ku dziko lapansi. Koposa zonse, anadzichepetsa kudzikaniza ku mphamvu monga Mwana wa Mulungu kulipira dipo loyenera chikondi. Mulungu akulamulira amuna kukonda akazi awo ndi chikondi monga chotere. Ndipo amafunitsitsa chikondi chotere chitakhala chokhadzikika mu Mpingo wake. Tiyeni tisankhe chikondi. Tiyeni tikonde monga umo Kristu anatikondera.

Abusa Sung-Hyun Kim 

Malichi 9, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Kondani Akazi Anu Monga Umo Kristu Anatikondera
Aefeso 5:25
Abusa Sung-Hyun Kim