Kristu Ndi Mpingo
(Aefeso 5:22-24)
Ubale wa Kristu Yesu ndi Mpingo woyera ndi wodabwitsa kwambiri komanso wa mtengo wapatali. Ndi maso akuthupi mpingo umaoneka ngati chinthu chopanda pake, monga ngati umo ukhalira nkumano wa anthu osowa chochita. Komabe, Mulungu anapereka kwa Yesu Kristu – Kukhala mutu wa zinthu zonse – kukhala mutu wa Mpingo woyera.
1. Mutu wa Mpingo
Yemwe ali Mutu wa zonse kuchokera pachiyambi pa zonse wakhaladi Mutu wa Mpingo? Nanga ndi zoona kuti Mpingo uli ndi ulemerero waukulu otere? Inde! Zoti Kristu Yesu ndi Mutu wa mpingo zimamangilirika ndi zokoma zomwe mpingowo uli, Kristu Yesu anapereka chilichonse kupulumutsa mpingo, monga iye ndi Mutu wake, Iye amayang’anira komasu kulamulira. Ndipo ndi mtima wokodwera mpingo umazipereka kumvera Iye.
2. Mpulumutsi wa Thupi
Monga Mpingo kumvera ndi kudzipereka kwa Kristu Yesu sichinthu choumilizidwa, koma mwa chilengedwa chathu tikungoyenera kumvera. Izi zili chonchi Chifukwa Yesu Kristu sali ngati m’mene aliri olamulira kapena ambuye ena onse omwe timawadziwa, Iye ndi modzi yekha yemwe anadzipereka yekha kukhala nsembe yamoyo ku Mpingo, ndi chikondi chopambana, chodzetsa chisangalalo. Pa chifukwa ichi nthawi zonse Mpingo umayesesa kuti uchite zomukodweretsa Iye. Umaika mtima kufuna kudziwa cholinga chake ndi miyoyo yathu ndi kuchita monga umo afunira. Ndipo nthawi zonse kuimbira nyimbo za matama kwa Kristu Yesu. Chiyembekezo cha Mpingo chamangililika mwa Kristu Yesu yekha basi.
3. Mwamuna ndi Mkazi wake
Pali njira ina yapadera yowonetsera ubale okoma pakati pa Kristu Yesu ndi Mpingo, ndipo uwu ndi ubale umene umakhala pakati pa mwamuna ndi mkazi wake. Mwamuna yemwe ndi ozozedwa ndi Mzimu Woyera amadzipereka kwathuthu kwa mkazi wake ndipo amachita izi kuti mkazi wake akhale okodwera nthawi zonse. Momwemonso, mkazi yemwe ndi ozozedwa ndi Mzimu Woyera amavera mwamuna wake. Iyeyu sachita izi chifukwa choti ndi udindo omwe Mulungu anamupatsa kuti adzitero monga mkazi, koma kuti potero amaonetsera kumvera Ambuye. Pamene mwamuna ndi mkazi akondana wina ndi nzake ndi kumverana monga m’mene Mulungu anakhazikitsira, khomo kapena nyumba yao sikhala monga m’mene nyuma zina zonse ziriri koma nyumba zawo zimakhala malo opatulika m’menemo cholinga cha Mulungu chimakwaniritsidwa.
Abusa Sung-Hyun Kim
Malichi 2, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Kumvera Amuna A Inu Eni Monga Kumvera Kristu
Aefeso 5:22-24
Abusa Sung-Hyun Kim