Kudzipereka Kwa Wina Ndi Nzake

(Aefeso 5:21)


Maziko okhazikika a ubale pakati pa anthu okhulupilira omwe Mulungu analamulira kwa okhulupilira mwa Yesu Kristu ndiko kukhala odzipereka kwa wina ndi nzake. Umu ndim’mene tiyenera kuchita monga okhulupilira Kristu ku mipingo kwathu, m’banja pakati pa amuna ndi akazi a iwo okha, pakati pa makolo ndi ana awo, komanso wolemba ntchito, ‘mbuyendi olembedwa. 

1. Kuchitirana ulemu ndi kudzipereka 
Kuchitirana ulemu ndi kudzichepetsa kwa wina ndi nzake kuposa ulemu omwe timapatsana kwa wina ndi nzake mwa chidzolowezi. Kulemekezana kumachitika molemekeza ma ufulu omwe tili nao pakati pathu. Kudzipereka kwatunthu munthu sayang’anira ma ufulu kapena udindo omwe ali nao. Ngakhale kuti mau oti kudzipereka kwa ena amamveka ngati onyazitsa koma ndi maziko amphamvu omwe amathandizira kuti anthu tikhale ndi moyo wa tsiku ndi tsiku pakati pathu mu umodzi. Palibe bungwe kapena dziko limene lingayende mu chipambano ngati anthu ake sagonjera kapena kudzipereka ku ulamuliro. Ichi ndi choonadi ngakhale mu mpingo wa anthu oyera mtima. Kotero kuti kudzipereka kwa wina ndi nzake pakati pa anthu okhulupilira Kristu ndi chinthu chofunika kwambiri, chifukwa chimathangatira kuti anthu afikire cholinga cha Mulungu pa miyoyo yao. 

2. Kudzipereka kwa mfumuUlamuliro 
Kudzipereka komwe Mulungu amanene sikwambali imodzi, koma kwa wina ndi nzake. Chitsanzo chabwino cha kudzipereka uku kumaonetseredwa pa nsembe ya moyo ya Ambuye Yesu Kristu. Monga Mfumu ya ulemerero wosatha mu ufumu wa Mulungu, koposa zonse, m’malo mwake adazipereka yekha kuti anthu ake apedze chisangalalo ndi chimwemwe kudzera mu kudzipereka kwake. Kudzera mu kudzipereka kwake tinalandira chipulumutso, motero tiyenera kukhala anthu odzipereka kwa wina ndi nzake. 

3. Kwa iwo azipereka kwa wina ndi nzake 
Akristu onse omwe ali ozazidwa ndi Mzimu Woyera ali ndi kuthekera kodzipereka kwa wina ndi nzake mopanda vuto. Ngati mwamuna akhumbira kuti mkazi wake akhale odzipereka kwa iye koma mwa mwamunayo muli chosalungama ndi chokhumudwitsa, izi zitsimikizira kuti otero ndi olephera pa udindo odzetsa moyo wa chisangalalo pa mkazi wa iye yekha, chimodzimodzi mkazi asamve mwa iye yekha kuphinjika pamene adzipereka kumvera mwamuna wa iye yekha. Kudzipereka mwa Yesu Kristu ndi udindo wa wina aliyense kwa nzake mosayang’anira mbali. Monga Yesu Kristu ngakhale anali ndi maonekedwa a Mulungu, koma anadziperekakapena kudzikhuthula yekha kwa Atate. Kudzipereka kwa mkazi kwa mwamuna wa iye yekha sikusonyeza kuti mwamunayo ndi opambana kwambiri kapena kuti mkaziyo ndi opanda pake, koma pali kusiyana kwa udindo wao monga mwa cholinga cha banja. Chidzalo cha mphamvu ya kudzipereka moona mtima chamangilirika mu chikondi cha Ambuye Yesu Kristu. 

Abusa Sung-Hyun Kim 

Febuluwale 16, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Ndi Kumverana wina ndi mnzace m’kuopa Kristu
Aefeso 5:21
Abusa Sung-Hyun Kim