KULEKANA PA UKWATI

(Aefeso 5:31-33)


“Nati, Cifukwa ca ici mwamuna adzasiya atate wace ndi amace, nadzaphatikizana ndi mkazi wace, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi? cotero kuti salinso awiri koma thupi limodzi.. Cifukkwa cace ici cimene Mulungu anacimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (MATEYU 19:5-6 – BUKU LOPATULIKA NDILO MAU A MULUNGU)

1. Sikunaloledwe
“Kodi Mose sanalamulire kupereka kalata wa chilekaniro ndi kumuchotsa? Inde, anachita izi. Komabe, sizitanthauza kuti Mulungu amakondwera ndi kulekana pa ukwati pakati pa mwamuna ndi mkazi wake.” Mu Baibulo, kulekana pa ukwati sizitanthauza kulekana kwa kuthupi kokha monga tichitira ndi ma ubale ena onse. Koma kumukaninzanso mkazi pa chosowa chake. M’chitidwe oipitsitsa ngati uwu udafalikira kwambiri. Chikadachitika ndi ciani anthu akanakana kuvomereza m’chitidwe umenewu? Azimayi osiyidwa akanasowa thandizo – kuchokera kwa amuna awo ngakhalenso anthu okhala nao pafupi.

2. Mu chikondi mulinso zowawa
Ngakhale mkazi atapazeka kuti wagwidwa ndi chigololo, Mulungu salolera kuti nkhani ya banja iwunikiridwe mwachisawawa. Umu ndi m’mene mtima wa Mulungu ulili pa ife; Pamene Hoseya, ali kusatira malamulo a Mulungu anatenga mkazi osakhulupirika kukhala mkazi wake ndipo anapitilira kumukonda ngakhale anali wokonda mchitidwe wa chigololo, mu izi anadzindikira kuzama kapena kupambana kwa kuwawa komwe Mulungu amamva pa chikondi chomwe ali naco pa Israyeli. Ndipo kuwawa uku ndi komwe Kristu amamva m’malo mwa Mpingo, momwemonso ifenso tiyenera kuvomeleza kumva zowawa chifukwa cha ena.

3. Ambuye anapilira m’masautso akulu
Tisanalingilire kubwenzera zoipa zomwe mkazi wachita. Pali chinthu chimodzi choyenera kulingalira bwino, monga kuona chosalungama cha mkaziyo mochifananiza ndi kuchuluka kwa ziopa zomwe takhala tikuchita pamaso pa Mulungu; Tiona kuti zoipa zomwe ena achitira ife nzochepa kuyerekedza ndi zomwe ife timachita pamaso pa Mulungu. Nthawi zonse timakhala ndi moyo chifukwa cha chisomo cha Mulungu, mwa chisomo chomwecho Mulungu amapilira mu zawawa. Ngakhale tikumva mkati mwathu, kuti tapilira mokwana, Mulungu wakhala muchipiliro kwakukulu chifukwa cha ife. Inde, zoona ndithu. Tinalandira chikondi chopambana kwambiri ndipo tikuchirandirabe ngakhale pano. Mwa ichi tiyeni tionesere chikondi mu moyo wathu. Tiyeni tionesere chinsinsi chachikulu cha Kristu pamene tivomeredza kukhala ndi ena mwa mtendere ngakhale tikudutsa mu nyengo zowawa.

Abusa Sung-Hyun Kim 

Malichi 30, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Chinisinsi Chachikulu Cha Kristu Chabisidwa M’banja
Aefeso 5:31-33
Abusa Sung-Hyun Kim