Kumvera Ambuye Anu
(Aefeso 6:5-8)
“Chifukwa ciani kuti ndimvere munthu? Ndimamvera Mulungu yekha.” Akristu ambiri amayakhula motero. Koma Mtumwi Paulo akuti, “antchito inu, khalani omvera ambuye anu – monga a thupi, mwa mantha ndi kunthunthumira, kuchokera pansi pa mtima monga kwa Kristu.”
1. Kumvera Kristu
Kwa akristu, Kumvera ambuye awo monga mwa thupi ndi mbali imodzi yomvera Kristu. Ngakhale makhalidwe a ambuyeyo ndi abwino kapena ayi, tiyenera kuwatumikira moona mtima ndi mokhulupirika. funso nkumati, “Ndingatumikire bwanji mbuye wanga moyenera? Ndingamusangalase bwanji? Makhalidwe awa umakhala ngati mbuli pakati pa anthu osakhulupilira, Koma zimapereka chilimbikitso kwa okhulupilira anzao komanso pamaso pa Mulungu, chimakhala ngati mbali imodzi yomutumikira.
2. Lamulo loperekedwa ndi Kristu
“Ine si wantchito wa munthu, koma wantchito wa Kristu; Ngati munena motero, ndipo mosimikidzira, uyenera kumvera ambuye ako akuthupi – Chifukwa kuchita ichi ndi kumvera lamulo la Kristu. Ngati ena ayesera kukondweretsa ambuye awo pamaso – munthu otero akhala ochita mwa thupi, Koma kumvera ambuye monga mwa thupi, ichi chisimikidzira kumvera Kristu.
3. Kristu adzapereka mphotho
Kugwira ntchito za ambuye awo mokhulupilika – m’malo moyamikira kumakunyoza poyera, uku kumakhala kuonesera khalidwe losowa umunthu. Tiyeni titumikire ambuye athu ndi mtima oona – kotero kuti mitima yathu ipezeke yangwiro ndi yokhulupirika pamaso pa Mulungu. Ambuye anu atha kukhala osakuyamikirani monga ndi m’mene mumaziperekera kungwira ntchito zabwino. Tiyenera kuthetsa kuvutidwa kwa mkati kapena kuwawidwa kwa mtima komanso kugonjetsa izi. Mulungu amadziwa chilichonse, ndipo adzapereka mphoto pa tsiku lachiweruzo. Kaya uli pa tchito yapamwamba kapena yapansi, palibe udindo kapena tchito ya muyaya – komanso izi zilibenso phindu pa chiweruzo chomaliza. Tiyeni tichoke pokhazikika ndi masomphenya opanda chiyembekezo kapena osaona patali, ndipo tigwiritse bwino ntchito mpata ndi nthawi yabwino yomwe tili nayo mu moyo uno.
Abusa Sung-Hyun Kim
25 Mayi, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Akhristu Omvera Ambuye Awo
Aefeso 6:5-8
Abusa Sung-Hyun Kim