Kumvera Komangilika Muchikhulupiliroa

(Aroma 1:5)


“Kodi sizoona kuti ngati ndikhulupirira Yesu, ndiye kuti ine ndapulumutsidwa? Ndiganiza kuti, kunenetsa motsimikidzira pa nkhani zokhudzana ndi kumvera, zimamveka pang’ono ngati kupanga Chilamulo kukhala cholemetsa. Ndithudi, kukhala mu moyo omvera ndi kwabwino ndithu, koma, kumvera kokha paokha sikufikitsa pakumangilirika ku chipulumutso. Sichomwecho? Ine ndili okhutira podzindikira kuti ndili opulumutsidwa sindisowekera kukhala pa moyo wa chikhulupiriro odzilemeretsa ndi zithu zina zambiri.”

1. Kusandulika mtima ndi Zoyenera kuchita
Okhulupilira ambiri amaganiza motere, Chilichonse, chimene Mulungu watipatsa ife kudzera mu Uthenga Wabwino sichili cha wamba mu chiombolo.  Uthenga Wabwino umabweretsa mwa ife kuthekera kuwiri, kusandulika mtima ndi zoyenera kuchita. Ndipo nthawi zonse kusandulika mtima kumabwera ndi ntchito yoti ichitidwe. Tinaomboledwa ku tchimo, ndipo tili ake a Yesu, mwaichi takhala olengedwa atsopano mwa kulandira moyo wa Iye. Mulungu waitana onse a ife, ndipo watitumidza kukagwira ntchito yake, Mulungu sapulumutsa munthu popanda kumupatsa ntchito yoti achite.

2. Kumvera komangilirika muchikhulupiliro
Titalandira zonse ziwiri, kusandulika mtima ndi zoyenera kuchita kudzera mu Uthenga  Wabwino, chomwe tisoweka kufuna ndi chikhulupiliro chomangilirika mu kumvera. “Buku la AROMA likuyamba ndi, “amvere muchikhulupiliro” ndipo mau oona akumalidza kuti, “kutsogozedwa mu kumvera kuwafikitsa mu chikhulupiliro,” Kumvera ndi chinthu mwa chilengedwe cha munthu chomwe chimasatira iwo omwe apulumutsidwa. Iwo omwe amakhulupilira mwa iwo okha koma kukana kumvera salandira chiombolo, chipulumutso chimaphatikidzidwa ndi kumvera, koma, chikhulupiliro chopanda kumvera sichikhalanso chikhulupiliro. Chikhulupiliro chomwe chimamangilirika mu kumvera ndi chikhulupiliro chomwe chitengera ku chipulumutso.

3. Ulamuliro obwera chifukwa chokhulupiliridwa
Ena m’kumati, “Ndimamvera Ambuye okha basi, osandiuza ine kuti ndimvere abusa.” Koma uku ndiko kudzitsutsa wekhawekha – Ambuye akuti, “Ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” ndipo “Dyetsa nkhosa zanga” M’kumati ine ndimayang’anilidwa ndi Ambuye, chonsecho ukukana kuvomeredza dongosolo la Mpingo kukananso ulangizi wa Abusa? Munthu otere amakhala motsogodzedwa ndi malingaliro ndi zokhumba za mtima wake. Ngati Uthenga omwe talandira uli choonadi chatunthu, tiyeni titsimikidzire ichi kudzera mu kumvera komangilirika muchikhulupiliro.

Okutobala 5, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
KUMVERA KOMANGILIRIKA MUCHIKHULUPILIRO
Aroma 1:5
Abusa Sung-Hyun Kim