Kupempherera Mbusa

(Aefeso 6:19-22)


“Pemphero la Mbusa? chabwino ….. koma pemphero langa lingathandize? Mbusa wathu ndi munthu oima molimba.” Munayamba mwaganizapo motere? Ngati ndichomwecho, Mbusa wanu akhala pa chiphyinjo kwakukulu pa yekha, popanda kuthandidzidwa kulikonse, mkati mwa nkhondo yowopsya ya uzimu

1. Pempho la Pemphero kwa Paulo.
Ngakhale uli mu unyolo, Paulo anapempha kwa anthu okhulupilira kuti amupempherere. “Phempherani kuti andipatse Mau, m’kunditsegulita m’kamwa molimba, kuti ndizindikiritse anthu cinsisico cha Uthenga Wabwino.” Paulo sanaike maso ake pa nyengo zoipa zomwe amadutsamo, mtima wake unakhadzikika pa kulalikira Mau, kwa iye, samasamalira za iye yekha – koma za Utumiki wa Uthenga Wabwino. Ndipo onyamula utumuki sanali Paulo yekha – koma oyera mtima onse omwe analandira chisomo cha Uthenga Wabwino.

2. Malingiliro a nkhondo a Satana.
Mbusa amakhala chindunji cha malingiliro a nkhondo ya Satana. Satana amadziwa bwino kwambiri kuti ngati akantha Mbusa, zotsatira zake nkhosa zibalalika. Amaonetsetsa kuti amupange Mbusa kukhala moyo wosinkhasikha, amagwa mukuziyeneredza kudziona ngati payekha ndiokwanira, kapena kuchita utumuki ndi zokhumba za iye mwini. Ngati apedza chipambano mu izi – ntchito ya Mbusa yokonzekeretsa okhulupilira kukhala angwiro mwa Kristu singathe kukwanilitsidwa. Munjira ina, pamene okhulupilira apempherera Mbusa, iye amatha kuima molimba motsutsana ndi zowawa  mu  kulimbika komwe Mulungu amapereka ndipo zotsatira zake, Mpingo umasungika. “kapena kutetedzeka”

3. Kupempherera Ufumu.
Ngati okhulupilira sapempherera Mpingo ndi Abusa awo, koma m’malo mwake kukhadzikika kudzipempherera iwo okha ndi zosowa za m’mabanja awo, mu kulingalira kwakuya, izi zili ngati kudzichotsa pa chisomo cha Mulungu chomwe anachibvumbulutsa mwa Iye yekha. Pemphero la kwa Mbusa silikhala la kwa iye yekha monga munthu, koma ili ndi pemphero lopita kwa oyera mtima onse – kuphatikidzapo ngakhale iwo omwe akupempherawo – ndi kwa Mpingo onse, ndi ku Ufumu wa Mulungu. Choncho, tiyeni ndi mtima wonse tipempherere Abusa athu. Tiyeni tibvomeredze cholinga cha Mulungu amene waitana ife mu njira imodzi, ndipo tiyeni tiime mu maitanidwe mwa chifundo ndi mokhulupirika.

Abusa Sung-Hyun Kim 

17 Ogasiti, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Kupempherera Mbusa
Aefeso 6:19-22
Abusa Sung-Hyun Kim