Kuthokoza
(Aefeso 5:20)
“Musaope kapena kudera nkhawa, m’mawa mukani kukaponyana nao nkhondo. Pakuti Ambuye ali nanu.” Pamene anamva kuti adani awadzera, mfumu ya Ayuda Yehosafati, anachita mantha. Koma pamene anamva mau ochokera kwa nneneri analimbikitsika mtima.
1. Kuthokoza Mulungu pa zomwe ukuyembekezera kuti zichitika
“Yamikani Ambuye, chifukwa chifundo chake ndi chosatha.” Mfumu Yehosafati analamulira gulu la nkhondo kupita kumalo komwe anakaponyana nkhondo ndi adani awo ndipo analamulira oyimbira Yehova kupita nao pamodzi. Ngakhale anali asanayambe kuponyana nkhondo, iye anali osimikizika mtima kuti apambana ndipo anayamika Mulungu. Kukanakhala kuti anayamika Mulungu atapambana nkhondo kale sibwezi chili chinthu cha mtengo wapatali kwambiri.
2. Kuthokoza chifukwa cha zomwe mwalandira kale
Inde, ngakhale kuti kuthokoza Mulungu pamene mwapeza chipambano ndi chinthu chabwino. Komanso ena sathokoza ngakhale atapeza chipambano. Amatenga chigonjetso mwa chizolowezi kapena mphamvu zawo ndipo sakhala ndi chifukwa chothokozera Mulungu. Izi zisiyana ndi anthu omwe amakhulupilira kuti chigonjetso chawo chimachokera kwa Mulungu, iye amathokoza, awa ndi odala. Koma pali odala koposa, onga uyu ali ngati Yehosafati, amathokoza pa zinthu zomwe akuziyembekezera kuchitika msongolo.
3. Kuthokoza ngakhale mutagonjetsedwa
Pali mulingo wapamwamba othokoza – monga kuthokoza Mulungu ngakhale palibe chipambano, ngakhale mukudutsa muzowawa za kulephera. Uku ndi kuzama m’chikhulupiliro, muyeso wa kuthokoza omwe Mulungu Atate amayembekezera kuchokera kwa ana ake. Ngakhale zikuoneka ngati chiyembekezo chatayika, Mulungu ndi oyenera mathokozo athu. Ngakhale zokhumba za moyo wathu sizikukwanilitsidwa, zizakwanilitsidwa monga mwa kufuna kwake, ndipo adzakwezedwa. Tilibe ufulu osankha kuthokoza kapena osathokoza, Mulungu nthawi zonse ayenera kuthokozedwa mosayang’anira nyengo zomwe tikukumana nayo.
Abusa Sung-Hyun Kim
Febuluwale 9, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Yamikani Nthawi Zonse Chifukwa Cha Zinthu Zonse
Aefeso 5:20
Abusa Sung-Hyun Kim