Lupanga La Mzimu

(Aefeso 6:17)


Masiku ano moyo ndi olimba – pamene wafika ku Mpingo  – uyenera kupumira pansi – kumva mtendere mkati mwako. Ndi chifukwa ciani umamva kulemedwa mkati mwako pamene ukumvetsera Mau a Mulungu? Sikoyenera kukhala odandaula kwambiri za tchimo kapena kulapa. Mulungu amakukonda ndi m’mene ulili. Chikhulupiliro sichitanthauza kudzilanga mwa iwe wekha – koma kuti zimathandizira kuti iwe ukhale chimene uli. Kotero tivomeledze ndi kutaya zonse zotitchinga mkati mwathu zolimbana ndi kusinthika.

1. Malemba monga Mau a Mulungu.
Kudzikaniza ku machenjerero a Mdierekezi, tiyenera kudzitengera lupanga la Mzimu. Talingalirani momwe njoka inafikira kwa Hava ndi kumufikitsa pokugwa ndi mau ochepa chabe omwe amamveka ngati abwino. Kuti timulake oipa mu machenjerero otere tiyenera kudziwa Mau a Mulungu. Izi sizitanthauza kudziwa Mau mwa pamwapa chabe. Tiyenera kulandira Mau omwe angatifulumidzitse ife – kutipulumutsa ndi kutitsogolera – mu mitima yathu – ndi kutikhadzikitsa mu chikhulupiliro molimba.

2. Chida chodzitetedzera.
Lupanga la Mzimu ndi chida chodzitetedzera, Iye amatithandidza kuima motsutsana ndi machenjerero a Mdierekezi ndi kulimbika. Ngati tinola lupanga la Mzimu moyenera, timakhala ndi kuthekera kopambana mayesero onga awa; “Kwalembedwa , Ndipo musafanidzidwe ndi makhalidwe a dziko lapansi, Koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu.” “Kwalembedwa,  kwa munthu wangwiro ku muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Kristu.”

3. Chida chopsya pankhondo.
Lupanga la Mzimu ndi chida chopsya pa nkhondo, ndipo nkhondo iyi silunjika pa Mdierekezi yekha – komansotu imagonjetsa tchimo lomwe iye amabweretsa – komanso ngakhale kwa ife, omwe timasenza udindo pa tchimoli – lupanga ili likafika pa ife, mitima yathu imabayidwa ndi chidzudzulo chake – koma tikatembenuka mbuyo mu nthawi yomweyo; ntchito zonse za Mdierekezi zimadulidwa ndi lupangali. Ndipo ndi mphamvu ya kumenya kwake – timasunthidwa – kuchoka ku m’chitidwe wa chinyengo kubwera ku choonadi, kuchoka mu m’dima kulowa mu kuunika, kuchoka ku tchimo ndi imfa kulowa mu chilungamo ndi moyo, kuchoka mu chisoni kulowa mu kukondwera, kuchoka ku nkhawa kukhala ndi chiyembekedzo, kuchoka pomangika ndipo kuyamba kukula, kuchoka ku umwana ndi kufika mu kukula mu chidziwitso, kuchoka mu kulephera kufika mu chipambano.

Abusa Sung-Hyun Kim 

3 Ogasiti, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
The Sword of the Spirit
Aefeso 6:17
Abusa Sung-Hyun Kim