M’bado Wapatsogolo
(Aefeso 6:1)
Kuti ana akule ndi moyo olungama, ayenera choyamba kutetezeredwa ku zoipa za dziko lapansi. Chifukwa tinabadwa m’chitidwe oyenda m’machimo. Ndipo nthawi zonse zotiyesa zikafika timadzigonjera. Chimakhala chiophyezo pa ana pamene makolo ao amakhulupilira kuti, “adzamudziwa Mulungu akadzakula.”
1. Njira ya m’dalitso
Kwa a Kristu, kukhala ndi ana ndi chinthu chamtengo wapatali kuposa umo anthu osakhulupilira Mulungu achionera. Pamaso pa Mulungu, sachitenga ngati ndi kungopereka mpata okhala ndi moyo padziko koma kukudza njira za m’dalitso. Ku mabanja omwe makolo alandira mdalitso la Mulungu ndi iwonso kupereka kwa ana ao, Mulungu amakwanilitsa cholinga chake chomwe ndi kupereka chipambano komanso kubwezeretsa umodzi mu ufumu mwa Kristu.
2. Malo omwe amakhala nao t’cheru
Satana amagwilitsa ntchito mzeru zakuya ku dziko lapansi kukhala njira yowonongera mabanja. Kukonda za dziko lapansi, kukhadzikika mu ziphunzitso za anthu, komanso kukhadzikika mu zinthu zina monga kukhulupilira kuti kulibe Mulungu. Izi zilipo kuti zichepetse ungwiro wa banja. kuononga ubale pakati pa makolo ndi ana awo. Kuwachotsa pa ulemerero wa Mulungu powapatsa ufulu osankha. Mwachizolowezi monga chule amasangalala mu phika ozazidwa ndi madzi, koma mapeto ake mphikawo ukaikidwa pamoto wambiri chuleyo amasanduka ndiwo, chomwechonso masiku ano mabanja akugwaigwa pang’onopang’ono mopanda kukhala ndi chidziwitso.
3. Cholinga cha Mulungu
Mulungu anati kwa Abraham, “kudzera mwa iwe ndi mbeu zako, mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsidwa.” “Pamene Israyeli amakhazikitsidwa, Iye anati, “udzakhala kwa Ine pfuko la ansembe.” Banja lirilonse liyenera kutenga udindo okhala wa nsembe.” Kuti cholinga ichi chikwanilitsidwe ku mbado ndi mbado, Israyeli adaika mitima yao kuphunzitsa ana ao mau a Mulunugu. Kaya kunyumba, kapena mu nseu poyenda, kaya pogona kapena podzuka. Kudzipereka uku kuyenera kupitilira ngakhale m’masiku athu ano. Pamene ana adakali ang’ono ndithu amakhala ndi kuthekera kophunzira mwansanga zikhalidwe za dziko lapansi. Tiyeni tisawapereke ku za dziko lapansi. Powaphunzitsa komanso kuwaonetsera za mau a Mulungu pamene adakali achichepere, Tiyeni cholinga cha Mulungu chipitilire kudzera mwa ife.
Abusa Sung-Hyun Kim
Epulo 6, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Mverani Okubalani Mwa Ambuye
Aefeso 6:1
Abusa Sung-Hyun Kim