Monga Matupi Awo
(Aefeso 5:28-30)
Monga mwachibadwa munthu alilera ndi kulisunga thupi lake. Ndipo nthawi zonse afunitsitsa kukhala wa thanzi labwino, kukhala owoneka bwino, komanso mwa ufulu. Inde, thupi silikanizidwa kukhala chomwe munthu akhumba mwa iye mwini. Umu ndi m’menenso Kristu achitira ndi Mpingo.
1. Kristu amasamalira ndi kutetedzera
Kristu amatitetezera ndi kutisamalira chifukwa ife tili ziwalo za thupi lace. Zofuna zake sizilingana ndi umo akhumbira wina aliyense monga mwa chipambano cha kuthupi. Chokhumba cha Kristu ndicho kuti tikhale thupi lake ndipo titengepo gawo pa cholinga chake. Mwaulemerero wake amadzipereka kuti Mpingo ukhazikike mu chipambano. Timalandira madalitso a Mulungu chifukwa ife ndi ziwalo za Mpingo, omwe uli thupi lake. Kristu ndi yemwe amazilumikidzitsa ndi Mpingo, amauzira mwa ife mpweya wa moyo, kukala nafe mu zowawa zonse, komanso kukhala nafe mu chisangalalo chonse.
2. Mwamuna asamalira ndi kutetedzera
Udindo ndi machitidwe omwe Kristu achitira Mpingo zifanana ndi umo amuna ayenera kuchitira akazi a iwo okha. Mwamuna ayenera kupereka zosowa za mkazi wake, komanso kupereka chisamaliro chokwanira. Mu chikondi chotere mkazi amapeza mtendere ndi chitonthozo. Koma ngati mwamuna amutenga mkazi wake ngati umo aonera china chilichonse chomwe ali nacho, namuchitira mosayenera, izi zikhala ngati kuononga thupi lake lomwe la iye mwini. Mwamuna yemwe ali m’chisomo cha Kristu ayenera kukhala n’dindo monga umo Ambuye ali, kwa mkazi wa iye yekha, monga umo Kristu awonesera ku Mpingo.
3. Osati monga m’mene alili katundu wamba – koma monga thupi lake lomwe
Kulemekeza mkazi sizifanana ndi umo monga wina achitira ndi zonse zomwe ali nazo. Kwa mwamuna, mkazi wake, ali ngati thupi la iye mwini, Kristu sanakweze mpingo kwa chabe, koma Mpingo uli thupi lake lenileni, ndipo ife tili ziwalo za thupi lake. Ife, omwe tinalibe kuthekera kotuluka m’matemberero osatha, tinalumikidzidwa kwa Kristu kukhala ziwalo zake. Pamene Kristu asamalira ndi kutetedzera ife, izi sapanga pachabe, Ichi ndi chikondi chomwe tinalandira. Tiyeni tionesere chikondi chonga ichi mu miyiyo yathu.
Abusa Sung-Hyun Kim
Malichi 23, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Kondani Akazi A Inu Nokha Monga Mukonda Matupi Anu
Aefeso 5:28-30
Abusa Sung-Hyun Kim