Mu Mzimu Wanga
(Aroma 1:8-10)
Anthu amatumikira Mulungu ndi zolinga zosiyanasiyana. Ena amatumikira mwa chilungamo cha iwo eni, ena chifukwa choopa kusalidwa ndi anthu ena, ena amatumikira kuti alandire ulemu kuchokera kwa anthu, ndi ena kufuna kuonetsera mphamvu zao, Koma chomwe Mulungu amafuna ndi mtima oona omwe umakhumbira kumusangalatsa Iye.
1. Zolinga za Kutumikira
Paulo anali munthu okhala ndi cholinga chabwino. M’dierekezi analimbana ndi Paulo kosalekedza kudzera mwa anthu ankafuna kumuletsa iye. Chonsecho Paulo sanaleka cholinga chabwino chinali pa iye, Chifukwa ubale wake ndi mulungu unali wabwino ndi osagwededzeka. “Kutsimikidzika mtima kwake kunali koti.” “Ndili ndi moyo chifukwa cha Ambuye yemwe anandituma ine!” Kudzera mu chidziwitso ichi chomwe anali nacho, amadzitenga ngati kuti ngakhale moyo wake ndi mphweya omwe iye amapuma zinali zake za Mulungu. Kwa Paulo, Kukhala mtumiki wa Ambuye odzipereka mwa iye yekha chifukwa cha anthu onse chinali chinthu chabwino kwambiri.
2. Undindo ndi Kukhulupirika
Nthawi zambiri anthu amati, “Ngati ine sindipanga izi, munthu wina aliyenseyo apanga,” Koma Paulo sanali chomwechi. Amaitenga ntchito ya Ambuye ngati ndi yake. Ngati kunali koti Uthenga Wabwino unalalikidwa mpaka ku dziko lonse lapansi, amakhulupilira kuti unali udindo wake kusenza ntchito imeneyi. Amapempherera mpingo kosalekedza ngakhale iye anali patali. Kufunitsitsa njira zokawafikira ndi cholinga chowatumikira iwo ndi kutsegula mtima wake konse mokhulupirika. Kukanakhala kuti zolinga zake zinali zotsogodzedwa mwa umunthu, mu nyengo zowawa ngati izi, sakanasankha njira zowawa ndi zopweteka ngati izi.
3. Ubale wa munthu ndi Mulungu
Paulo monga munthu, amakhulupilira kuti kusunga malamulo ambiri mwathupi ndi njira yotumikira Mulungu. Koma mkati mwa Uthenga Wabwino, anasandulika m’modzi yemwe anatumikira Mulungu ndi mzimu wake. Kwa iye, chinali chofunika chinali chopotsa kukhala olungama chifukwa iye anakhadzikika kwambiri – chinsisi chake chinali ubale wake ndi Mulungu. Kudziwa mtima wa Mulungu ndi kupereka moyo wake mwakufuna kwa mtima wake kwa zomwe Iye akodwera nao – Ichi Chikhale cholinga cha machitidwe a utumiki wake kwa Mulungu. Chomwecho ifenso, tili mu Uthenga Wabwino lero, ndi mzimu wathu, ndi kukhulupilira, tiyeni titumikire Mulungu.
Okutobala 19, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Mulungu amene ndimamutumikira ndi mzimu wanga
Aroma 1:8-10
Abusa Sung-Hyun Kim



