Munthu Ali Kakasi Kufuna Uthenga Wabwino

(Aroma 1:21)


Chifukwa chimodzi mwa zambiri chomwe munthu sadzapulumuka ku mkwiyo wa Mulungu ndi chakuti munthu amakana Mulungu. Kumukwedza Mulungu ndi chinthu chabwino choyenera kwa zolengedwa zonse, chili ngati chamangawa kwa Mulengi, Koma chonsecho munthu amadzikanidza ku dongosolo lomwe linakhadzikitsidwa kuchokera pa chiyambi.

1. Wosathokoza Ndipo Malingiliro Awo Ali Oipa
Ngakhale anthu amalandira nasangalala ndi zonse zochokera kwa Mulungu, mwakuuma mitima yao amakhala akumukana Iye. Kukhala osathokoza, alibe kuthekera koti chikhulupiliro chimere mizu, komanso kuthekera kokhala ndi chikhulupiliro kumakhala kutali. Kukana Mulungu ndi kukana choonadi chapatali choposa chinthu chilichonse ku dziko lonse lapansi. Kudzera mum’chitidwe otere, mukusawerengera kuti amalimbikira motani, malingiliro awo sangafikire ku choonadi, m’malo mwake amalamuliridwa ndi zokhumba za matupi awo, mopanda kusankha iwo amasatira chomwe chili choipa.

2. Mitima Yao Inadetsedwa – Kuwalondolera Mukuchita Zoipa
Pamene anthu akhutira ndi uthenga onyenga omwe dziko lapansi lipereka ndi machitidwe oipa akhadzikika pa ichi, mitima yao imadetsedwa. Zotsatira zake, kuchitachita kwa Mulungu sikupedzeka mwa iwo, ndipo mphamvu ya tchimo imakula kwakukulu. Vuto ili silingathe chifukwa choti wina wapedza chidziwitso cha za uzimu. Pamene mtima wadetsedwa munthu alibe kuthekera koona tchimo ngati tchimo, m’malo mwake, chidziwitsocho chimamulondolera ku njira yoipa kwambiri ndi yonyenga. Mapeto ake, Chodetsa chauzimu chimamutengera ku chosalungama chonse, ndipo kudzera mumakhalidwe otere, ntchito zoipa zonse zimazionetsera zokha mwamunthuyo.

3. Kulephera Kulemekedza Mulungu Ndi Kumukana Iye
Mosiyana ndi zolengedwa zonse, munthu yekha amalephera kumulemekedza Mulengi ndi kumukana Iye. Apa ndi pamene pagona chifukwa chotsimikidzira kuti munthu sadzapulumuka ku mkwiyo wa Mulungu. Lero, munjira iliyonse, kudzera mu nsembe ya Kristu, talanditsidwa ku mkwiyo wa Mulungu. Motero tiyenera kulimbika kutaya machitidwe athu okana Mulungu. Muzinthu zonse, tiyenera kumulemekedza Mulungu ndi kuthokoza pa zonse zomwe amatipatsa. Tiyeni tikane choipa cha dziko lapansi ndiko kulingalira zoipa ndi kukozanso kwa mitima yathu m’choonadi. Tiyeni tisalolere kuti mitima yathu idetsedwe, koma kuti idzadzidwe ndi Ambuye.

Zitunda 7, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Anthu amakana Mulungu
Aroma 1:21
Abusa Sung-Hyun Kim