Mwana wa Mulungu

(Aroma 1:3-4)


“Ndiye kuti ciani – mukunena kuti Mwana wa Mulungu sanabwere ku dziko lapansi chifukwa cha ife? koma kuti anabwera chifukwa cha zolinga zina, ndipo chifukwa choti anali pano – zotsatira zake anapulumutsanso ife? Chabwino, ndikhulupilira kuti ichi chinachitika mwa mwai chabe, kotero kuti tinapedza chipulumutso.”

1. Chifukwa chomwe anabwerera mwa thupi
Iye amene anali ndi maonekedwe a Mulungu anabwera m’thupi ndipo anaika chisomo pa ife, Iye amene sadadziwe tchimo anasenza machimo athu – ndipo anapachikidwa pa mtanda, kufikira imfa. Koma ngati mau awa achokera pa milomo yathu, tingakhale onena zoona kuti timadziwa Uthenga Wabwino? Chifukwa chomwe Mwana wa Mulungu anabwerera ku dziko lino lapansi ndi chodziwika bwino lomwe ndithu. Anabwera kupereka moyo wake chifukwa cha anthu ambiri. (Monga Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wace dipo la anthu ambiri. – Mateyu 20:28)

2. Kusandulidzika kwathuthu
Iye amene anali ndi maonekedwe a Mulungu anakhala wa thupi – osati chifukwa chodzichepetsa chabe pamaso pa Mulungu, koma kuti apulumutse ife. Chipulumutso chathu sichinachitike ngati mwangozi – kapena kuti zochitika mwa mwai zomwe zinamutengera kuifa ya thupi. Anabwera kuti tilandire moyo wa Mulungu, kotero kuti tikamasulidwe ku zowawa ndi zokhumudwitsa, zochokera ku tembelero ndi imfa. Ndipo izi zinabweretsa moyo wosatha, kusandulidzika kwathuthu. Iye anabwera kutipatsa ife moyo.

3. Chikondi chinabwera pa ine
Pamene Iye amene anali ndi maonekedwa a Mulungu anakhala wa thupi kudzera ku mbeu ya Davide monga mwa uneneri, Umwana wake unalongosoleredwa bwino mu zolembedwa. Ichi sichinachitike mwakukwanilitsa lonjedzo loperekedwa kudzera kwa aneneri kokha, Chipulumutso chathu si mwai chabe –  ichi ndi chipatso cha chikondi cha Mulungu. Tiyeni tisatenge chikondi ichi mopepuka. M’malo mwake, tiyeni tidzindikire chomwe ife tili kudzera mu kubvomeredza za izi. “Mwana wa Mulungu anabwera chifukwa cha ine” ndi mitima yathu kuikhadzikitsa mu chidzindikiritso cha chikondi choposa kuti anasiya zonse chifukwa cha ife. Tiyeni timulandire Iye ndi umunthu wathu onse.

Abusa Sung-Hyun Kim 

Septemba 21, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Mbewu ya Davide, Mwana wa Mulungu
Aroma 1:3-4
Abusa Sung-Hyun Kim