Ntchito Za Opulumutsidwa
(Aroma 2:6)
“Zilibe kanthu kuti ngakhale timachimwa kapena kuchita zabwino, chifukwa tinapulumutsidwa kale, chiwerudzo chilibe gawo pa ife, mwa ichi moyo wanga sangalala.” Akristu ambiri samvetsetsa Mau, “Okhulupilira Iye sawerudzidwa.” (YOHANE 3:18) Malingaliro oipa omwe anthu opita ku Tchalichi mwachidzolowezi anapatsidwa ngati chiphatso chaulere chowafikitsa ku mpando wa chiwerudzo.
1. Omwe Ayembekedzera Chiwerudzo
Tsiku la mkwiyo ndithu lidzafika. Tsiku ili la chiwerudzo chomaliza lidzabvumbulutsidwa pamaso pathu pakufika kwa Yesu Kristu. Siosakhulupilira okha omwe adzaona tsiku limeneli, Malemba akuti oipa onse omwe samakhulupilira Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu ndi ochita kusawerudzika ndi omwe ali m’kuyembekedzera chiwerudzo. Pamene anthu ali kuyesera kusiyanitsa munthu opita ku Tchalichi ndi osapita ku Tchalichi, choona chenicheni ndi chakuti munthu wina aliyense amakhala m’moyo osiyana.
2. Muyeso Wa Chiwerudzo
Chiwerudzo chidzaperekedwa kwa munthu wina aliyense monga mwa ntchito zake. Aneneri mu Chipangano Chakale ananena za ichi, momwemonso Yesu akuti, “Ndidzapereka mphotho kwa munthu wina aliyense monga mwa ntchito zake.” Mtumwi Paulo anati, “Kotero tonse tidzaimilira pa mpando wakuwerudza wa Kristu, kotero aliyense adzalandira kuchokera ku ntchito zomwe anachita mwakuthupi…… kaya zabwino kapena zoipa. (2 AKORINTO 5;10) Analalikira za chisomo cha chipulumutso m’moyo wake onse, koma ananenetsa kuti opulumutsidwa adzawerudzidwanso monga mwa ntchito zao.
3. Machitidwe Aumulungu
Chipulumutso timalandira kudzera mu chikhulupiliro, koma chitsimikidzo choti wina anapulumutsidwa chimaonetseredwa kudzera mutchito zao. Anthu ambiri amachepsya ntchito koma amayankhula kwambiri za chisomo chifukwa choti amasokonedza ndi zoyeneredza za chipulumutso ndi muyeso wa chiwerudzo. Chipulumutso ndi chachisomo koma chiwerudzo monga mwa ntchito za munthu. Tiyenera kuyankhula bwino za chisomo kuti wina asazitamandire, koma sitiyenera kukana cholinga cha Mulungu cholenga ife kuti tichite ntchito zabwino. Machitidwe athu aumulungu amakhazikika kuti chokhumba cha Mulungu chikwanilitsidwe ndipo chizalemekeze Iye.
Abusa Sung – Hyun Kim
Febuluwale 8, 2026 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Adzapatsa Aliyense Monga Mwa Ntchito Zake
Aroma 2:6
Abusa Sung-Hyun Kim


