Uchitsiru wa Munthu
(Aroma 1:22)
Munthu amadzitenga ngati wanzeru payekha, kudzitenga ngati ofikira ku choonadi mwakuyetsera ku nzeru ya umunthu, Pa choonadi, muzonse akuyenda munjira yoipa, atapambukira pa chilungamo chenicheni. Ngakhale ali ndi chidziwitso chonse cha Mulungu oona, asinthitsa choonadi cha ulemerero wake chosawonongeka ndi kufananiza ndi cha munthu chowonongeka.
1. Kupita Chitsogolo? Ayi, Kubwerera Mbuyo!
“Ndimakhulupilira mu mphamvu ya kulingalira, kalekale pamene anthu anali pa umbuli, ankadalira zikhulupiliro zamakolo. Koma pamene anatuluka mu umbuliwu anasintha zikhulupilirozi kukhala ngati dongosolo la chipembedzo, natenga izi ngati zinthu zomwe zili ngati zapamwamba mu chipembedzo.” Munthu amakhulupilira kudzilungamitsa ndi mphamvu za umunthu, koma pakusatira mbiri yakale zikuonetsera mosiyana, Matsiku akale Roma ndi Greece, pakati pao panalibe mafano onga amaonekedwa a nyama, kapena a munthu. Baibulo likuonetsera kuti asanafike komanso ngakhale nthawi yomwe chigumula cha Nowa chitachitika kumene, mchitidwe opembedza mafano kunalibe. Munthu anali kuyenda mu moyo wa njiru – moyo oyenda modetsedwa pamene anapatuka kwa Mulungu oona nayamba kupembedza zinthu zina.
2. Kuchokera Ku Nzeru Ya Chidziwitso Cha Chirengedwe? Ayi, Zokometsera Za Nzeru Ya Munthu!
Munthu amayetsera kutanthauzira zinthu zonse mwakulingalira kwa umunthu osati choonadi, modzitukumula mwa chidziwitso cha nzeru za iwo eni. Chonsecho, muyeso wa moyo wao wakhadzikitsidwa pa malingaliro omangilirika ndi mphamvu ya kuthupi lachivundi ndikufikira kulephera kuonetsera choonadi chauzimu. Zotsatira zake, munthu satha kubvomeledza za kukhadzikika mu moyo wa uchimo. koma m’malo mwake kudzilungamitsa muchoonadi cha iwo okha. Mulungu amawatenga anthu otere ngati “zitsiru” Kumvetsera mu nzeru ya Chidziwitso cha chibadwidwe – kuyetsera kufotokodzera mokometsera kudzera mu maonekedwe auchitsiru chonsecho akudzikanidza ku chobvumbulutsidwacho – ichi chili chabe kudziyeneredza kopanda pake.
3. Kutsatira Mau a Mulungu? Ayi, Kutsatira Zokhumba za Anthu!
Timabvomeledza kuti timakhala mosongozedwa ndi Mau a Mulungu, koma kodi izi sikungoyankhula ngati zoona koma zili nzeru zochokera ku umunthu? Sititenga ichi monga ngati cholowa chomwe tapedza kudzera mu mphavu yakuthupi, kutchuka, ndi zokhumba za mitima yathu kudziika malo omwe Mulungu ayenera kukhala? Mulungu yekha ndiye amene ayenera kukhala Mbuye wathu, Chokhumba cha miyoyo yathu ndi kuunika kotsogolera pa njira yathu, kufuna choonadi cha Mulungu chokha ndi kuphunzira kwa Mau a Mulungu, ziyenera kukhala madziko okhadzikika a kaganidzidwe kathu ndi m’kono oona utsogolere miyoyo yathu ku moyo wosatha. Ndichokhumba cha moyo wanga kuti Mulungu yekha akhale nsanamira ya miyoyo yathu ndi chilichonse chathu.
Zitunda 14, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Chibadwa cha Munthu Chosinthana Mulungu ndi Mafano
Aroma 1:22
Abusa Sung-Hyun Kim


