Udindo Wa Makolo
(Aefeso 6:4)
Ana sali ngati katundu kwa makolo awo – mwini wake ndi Mulungu. Ngati makolo achikana ichi ndi kuyankhula kapena kuchita mosasamala – kuonesa monga mwa thupi makhalidwe ena mopanda kulingilira bwino – ana ao amavuladzidwa m’mitima. Zotsatira zake – njira ya mitima yao yomwe imalumikidzitsidwa ndi Mulungu imaduka.
1. Chikondi chenicheni
Kuophyeza koonjeza ndi malire ena – omwe amapangitsa kuti ana amve kuti sakulemekezedwa monga anthu – kuchita zinthu zosiyanitsa pakati pao ndi kuonetsa kukondera kwa ena, kuwaumiriza kuchita zinthu mosalemekeza kuthekera kwao – kuwalera mopanda kuwalemekeza, makhalidwe abwino, ngakhale kusavomereza zabwino zomwe iwo ali – izi zimakhazikika mu mtima wa mwana ndipo zimawapatsa mkwiyo waukulu. Mkwiyo uwu sumaoneseredwa kudzera mu kuyankhula koma nthawi zambiri zimaonekera pamene ataya chiyembekezo komanso kuonongeka kwa ubale – ndipo pamapeto pake – zimatha kubweretsa chiophyezo ndi chionongeko ndi Mulungu.
2. Kuwunikira m’chikhalidwe ndi malangizo
Makolo ayenera kuwaphunzitsa chikhalidwe ana ao mwa chikondi kudzera pokhala ndi nthawi yowaphunzitsa mau a Mulungu, Monga ndi cholinga cha Ambuye kutero. Kudzera mu izi atha kusogolera ana ao mu makahalidwe oyenera Mulungu. “Ngati ena apanga mobisala, inunso mutha kutero,” monga lichitira dziko lapansi kapena kuti anthu onse, mchitidwe onga uwu umapangitsa kuti ana achoke pamaso pa Mulungu. Chomwe ana amayembekezera kuchokera kwa makolo ao ndi upangiri wabwino omwe ungawafikitse kwa Mulungu okhulupirika ndi oona.
3. Mtima olapadi
Ena amamva kuwawa mumitima yao chifukwa cha zitonzo zomwe zimadza chifukwa ana sanawakudze molingana ndi cholinga cha Mulungu. Izi ziyenera kutero ndithu, sitingazikane. Komanso motero tiyenera kukhala anthu osimikizika mu mtima kukhala anthu ofunitsitsa kulapa machimo athu nthawi zonse. Kuyambira pano kupita msogolo, tifunitsitse kukhala ngati manja a Mulungu pakati pa ana athu – ndi onse omwe Mulungu watipatsa omwe asowekera chikondi chathu. Ngakhale zikuoneka kuti tidalekerera, chilipo chiyembekezo kuti kuthekera kulipo kuti titha kuchita bwino. Kulapa kwathu – kuikapo mtima kuti tisinthe – komanso machitidwe oona ndi okhadzikika monga tikhalira zitha kuthandizira moyo wina kukhala okhudzika kufikira muyeso wina wabwino. Mulungu agwiritse ntchito zimenezi ku tchito yake yabwino.
Abusa Sung-Hyun Kim
11 Mayi, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Musayambitse Ana Anu Ku Ukali
Aefeso 6:4
Abusa Sung-Hyun Kim