UMBONI WA MKATI MWANGA
(Aroma 1:19)
Palibe munthu pa dziko lino lapansi yemwe atha kunena kuti sakudziwapo kanthu kalikonse zokhudza Mulungu. Mulungu mwini anaika mwa munthu wina aliyense umboni wabwino oti wina aliyense akhale ndi chidziwitso cha Iye.
1. Chibvomeredzo Cha Helen Keller
Umboni wa m’kati ndi wamphamvu kwambiri kotero kuti umawalitsa ngakhale njira za chidziwitso zatsekeka. Helen Keller – yemwe anali osapenya komanso osamva anachitira umboni za izi. Pamene mlongo Sullivan anayamba kumuwuza iye za Mulungu, Helen anati, “Ndinamudziwa kale Iye, chomwe sindimadziwa ndi dzina lake lokha.” Ngakhale chidziwitso chinali chisanaululidwe pa iye, mzimu wake unali ndi kuthekera kodziwa Mulungu wake.
2. Kudzipatsa Danga Lakumva Tchimo Kukoma
Anthu akamati sakumudziwa Mulungu, sichifukwa choti alibe kuthekera komudziwa Iye. Amakana kuwala komwe kuli mwa iwo ndi cholinga choti azimva kukoma tchimo. Kumayerekedza ngati samudziwa Mulungu ndi cholinga choziyeneredza ndi kuyenda mu moyo wosogozedwa ndi zokhumba zawo. Kuwala kunafika kale mwa munthu wina aliyense, kotero kuti kukoma kwa tchimo kumawachotsa anthu ndi kuwabisira mu kuwala ndi mphamvu zao zonse. Moyo onga uwu uli pa mavuto akulu.
3. Moyo Ogwiritsa Mavumbulutso
Ngakhale kwa iwo omwe amayenda mu chikhulupiliro chakufa amavomeredza ndi kukhala ndi mantha a chiwerudzu chake, ndiye tichita motani – ndani walandira chikondi cha mtanda ndi Mau a vumbulutso – ndikukhala ovomeredza? Tili ndi ngongole ndi Mulungu yomwe sitingakwanitse kubwenza, tsono tiyeni titaye kudziyeneredza mwa ife tokha – kukaikira kulikonse komwe kumatitsogolera pa kulungamitsa tchimo, ndi kulandira mavumbulutso ndi kukhulupilira koona – Tiyeni tilandire chikondi chomwe chinapatsidwa kale kukapulumutsa ife – ndi kulemekedza Mulungu – osati mwa mantha, koma ndikukondwera kwakukulu ndi chiyamiko.
Novembala 23, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Umboni wa Mulungu Wobzalidwa mwa Munthu
Aroma 1:19
Abusa Sung-Hyun Kim



