Nthawi ya Kuchenjedzedwa

(Aroma 2:5)


Anthu ambiri lero amatenga chilungamo cha Mulungu kukhala chopepuka ndi chiyembekedzo chonse amaona ngati  chiwerudzo sichidzabwera. Achita ichi chifukwa amaona kuti palibe chimachitika nthawi yomwe achimwa, amaganiza motero. Kotero ubwino wa kukhululukira kwa Mulungu kudzaoneka ku chilungamo cha imfa ndi chionongeko chachikulu.

1. Tchimo Lopelekana – Kuzengeredza Za Kukhululukidwa
Ubwino wa Mulungu, kulekerera ndi kupilira zili zowawa zomwe amazivomeredza pa ochimwa. Mwanjira ina ngati tidzikanidza ku chisomo chapadera kukhala ngati mpata okanira kulapa, chimakhala choipa machitidwe akukana ndi kuponderedza kukhulupirika ndi chifundo. Pamene tikukana ubwino wa Mulungu, ndi pamene tikunyalanyadza mu uzimu ndipo mukutsutsidwa kwakukulu ndi liwiro loposa, Uchimo okhadzikika kwa nthawi yaitali uwu utitengera udindo waukulu wa miyamba kuposa tchimo lililonse lakuthupi.

2. Kuumitsa Mtima – Kuzima Moyo Wauzimu
Kuumitsa kwa mtima ndiko kuima motsutsana ndi kukondera kwa Mulungu zimapha, “kuzima moyo wauzimu” chimakokera moyo ku Gehena. Mbiri ya a Israeli ili m’machitidwe ochita mobweredzabweredza a kuumitsa mtima komwe kuli kuchita motsutsana ndi kuledza mtima kwa Mulungu izi zibweretsa zowawa pa Iye. Ngakhale Yesu, yemwe anachita chifundo pa ochimwa, anaona kuuma mtima kwawo anakana kulapa nthawi ya chifundo ndi chisoni ndi mkwiyo. Kuumitsa mtima ndi muzu wa choipa omwe ulunjika motsutsana ndi ubwino wa Mulungu.

3. Kuchulukitsidwa Kwa Mkwiyo Ndi Chiwerudzo Chomwe Chidza Posachedwa
Chifukwa choti chilango sichisatira pamene munthu wachimwa, sizitanthauza kuti udindo pa tchimo wachotsedwa, munthawi yomwe mitima  iuumitsidwa machitidwe opanda chikumbumtima mkwiyo owopsya wa Mulungu uli kuchulukitsidwa molingana ndi machitidwe a anthu ku nyumba zosungiramo zosaoneka ndi maso za muyaya. Patsiku ilo pamene chiwerudzo cholungama chidzabvumbulutsidwa pa onse owme akhala ali mu moyo wa chiwerudzo chosalungama. Pamene tili ndi mwai uwu lero, tiyeni tiphwanye kuuma kwa mitima ndi kubwerere kwa Yesu Kristu yemwe atipanga ife kukhala atsopano, kupedza njira ya moyo.

Abusa Sung – Hyun Kim

Febuluwale 1, 2026 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Kuuma Mtima Kusungira Mkwiyo
Aroma 2:5
Abusa Sung-Hyun Kim