Akuchita Mau
(Aroma 2:13-16)
Palibe yemwe ali opatulidwa ku chiweruzo cha Mulungu. Ngakhale pa yemwe analandira Mau kapena osalandira, aliyense azaima monga mwa muyeso omwe unaperekedwa pa iwo. Kudziwa Mau mwachindunji sizitanthauza kuti pali mwai oti wina sadzaweruzidwa. Pachifukwa ichi tinena kuti anthu olungamitsidwa ndi Mulungu siomwe ali a kumvaimva Mau kokha, komanso iwo ochitachita mwa Mau.
1. Ubwino Ochita Mau
Lero, akristu ambiri amakhala pansi kumvera Mau a Mulungu ngati umo zikhalira onerera mukalasi. Amamvetsera osatengapo udindo, amakhala ofuna kumvetsetsa monga mwa kuya kwa zokhumba zawo. Momwemonso, ngati wina amvaimva Mau koma kukana kuyendamo, chidziwitsocho chidzaima ngati chomuyesera pa tsiku la chiwerudzo. Kwa munthu yemwe ali ndi kuthekera kwakumva Mau mozama iyeyu undindo wa mulandu wake uzakhala waukulu kwambiri. Kumvaimva Mau koma osachita, ichi pachokha ndi machitidwe akusamvera.
2. Palibe Amene Ali Mfulu Pa Nchito Zake
Muyeso wa chiwerudzo suzakhala kwa anthu omwe analandira Mau okha, Mulungu anaikiratu muyeso mu mtima wa munthu aliyense. Ichi ndi chifukwa chake anthu ali ndi chikhalidwe chotsutsana ndi chosalungama, ndikutembenuka kuleka choipa, nachitira chifundo kwa omwe ali m’mavuto. Pachifukwa choti amalingalira ndi kuchita mokoma motere, izi zitsimikidzira kuti muyeso wamkati mwao uli wamoyo. Kotero, chifukwa ali ndi kuthekera kodzindikira chabwino koma anakana Mulungu yemwe analemba izi, ntchito zawo zabwino zizaima ngati umboni wakuwatsutsa patsikuli.
3. Amawerudza Ngakhale Malingaliro Amkati
Ngakhale ndi maso akuthupi ntchito zabwino zimabvumbulutsidwa za machitidwe abwino pa Mulungu. Koma Iye amayesa zokhumba za mitima molingana ndi mayendedwe. Chokhudza kwambiri ndi ichi, monga mwa chilengedwe, “mophatikidzana ndi chidziwitso” chidziwitso champhumphu pakati pa Mulungu ndi iwe mwini, chimaima ngati uboni osatsutsika. Ngati tidzikanidza ku choonadi, kukhudzika mkati mwathu kumadzilala. Koma ngati tilimbika kuima mokhulupirika pamaso pa Mulungu, timadzindikira malire athu ndipo timagwa pa mapazi a Kristu. Tiyeni tisakhale oyesera, “kutsogolera” Mau – koma ife tikhale otsogoleredwa ndi Mau pamaso pa Mulungu.
Abusa Sung – Hyun Kim
Lachiwiri 8, 2026 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Lamulo Lolembedwa Mumtima
Aroma 2:13-16
Abusa Sung-Hyun Kim



