Ntchito Ya Tchalichi

(Aroma 2:17-20)


Mulungu anakhulupilira Ayuda ndi ntchito yopita ku dziko lonse lapansi. Anaikidwa kuti agwiritsidwe ntchito mu mbiri ya chiombolo pa kubwezeretsa pa kugwa kwa anthu ndi kukhadzikitsidwa ngati njira yobweretsera mdalitso kwa mitundu yonse kuti idalitsidwe. Koma analephera. Tsopano ntchito yapatsidwa kwa ife – Tchalichi cha Yesu Kristu.

1. Maziko Achitetedzo
Ayuda ankakhulupilira kuti ali otetedzedwa ku chiwerudzo chifukwa chabe choti iwo ali anthu osankhidwa a Mulungu ndi opatsidwa chilamulo. Koma anasiya padera Malemba nakhala odzitamandira mwa Mulungu, anachititsa maso awo kukhala akhungu pa choonadi chomwe Iye amachiyembekedzera. Nneneri Mika ananena za chionongeko chachikulu cha Yerusalemu kwa iwo olandira chokometsera mulandu ndi kupereka uneneri mofuna ndalama, chonsecho kulephera kuvomeledza chonenedwa chakuti, “Kodi Ambuye sali pakati pathu! Palibe choipa chidzagwa pa ife! kukhala ndi dzina kapena kutengapo chidziwitso mwandera, popanda chotsimikidzira cha chitetedzo. Tiyeni choyamba tidzifunsa, “Kodi maziko enieni a chitetedzo changa ndi ciani?”

2. Kusiyanitsa Kudziwa Ndi Kulekerera
Mtumwi Paulo akubweretsa zozitamandira zowatsutsa zinthu zinai zomwe zili udindo wauzimu zomwe Ayuda ayenera kudzitamandiramo, Kulondolera munthu wakhungu, nyali kwa amene ali mumdima, wolongiza wa opanda nzeru ndi phunzitsi wa tiana. Izi zinali ntchito zamtengo wapatali zomwe Mulungu anakhulupilira pa iwo. Koma, m’malo mosogolera amitundu ku cholinga cha Mulungu choona, Ayuda anakodwa mu machitidwe a chikhalidwe otsokera. Zotsatira zake, anapangitsa anthu omwe anawatembenudza mitima ngati mwana kutsokera kwakukulu mobweredza muyeso wakale kukhala ana aku Gehena. Momwemonso kwa iwo, mwapamaso kudzionetsera ngati aumulungu. Pamene kudziwa sikuonetseredwa mu kulekerera. Chidziwitso sichikhalanso chokhadzikika pa chiphunzitso ndipo chimakhala m’malo mwake muyeso woyesera chiwerudzo.

3. Phunziro Kuchokera Pa Kulephera
Maganizo odzipatsa chitonthozo omwe amati, “Za ine zili bwino chifukwa ndimapita ku Tchalichi ndipo ndimadziwa Baibulo,” amafana ndi chikhadzikitso cha kunyalanyadza kwa Ayuda. Mulungu samawayetsa atumiki ake ndi muyeso wachidziwitso chawo, koma kuzama mukumvera komanso kusandulika kwa miyoyo yawo, Komanso chenjedzo ili silithera pa kudzudzula kokha, Ambuye amatigwilizitsa ife ndi kwa munthu aliyense amatitsogolera kuti tisasatire machitidwe awo. Amatichotsa ife posakasaka zinthu zakuthupi kuti tikhale omvera, kuchoka mochita mderadera kufikira ku choonadi, kuchoka podzitamandira kufika potumikira. Ntchito yomwe Ayuda analephera kukwanilitsa, iyenera tsopano kugwiridwa ndi ife, monga Tchalichi.

Abusa Sung – Hyun Kim

Lachiwiri 15, 2026 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Anthu Omwe Alephera Kukwaniritsa Udindo Wawo Wolandira Chivumbulutso
Aroma 2:17-20
Abusa Sung-Hyun Kim