Chikhulupiliro Chopanda Chilungamo

(Aroma 2:21-24)


Chopindulitsa ndi ciani pamene palibe kusintha m’moyo ngakhale mumanena kuti mumakhulupilira? Munthu yemwe anakumana ndi Yesu muzenizeni, mwa iye mumakhala kusintha kwakukulu ndi mbiri yosandulidzika mtima ya miyoyo. Tonse, omwe tinamva ndi kuphunzira ndi kuphunzitsidwa Mawu – tiyenera kuima moona mtima pa funso lobaya mtima ngati ili.

1. Kusiyana Kodziwa Ndi Kukhala Muchimenecho
Ayuda akale anali odzitamandira chifukwa analandira ndi kuphunzitsidwa chilamulo. Ngakhale miyoyo yao inalunjika kuchionongeko chachikulu mwa mphamvu yosaneneka, anaima muchikhulupiliro chosasunthika kunena kuti ku uzimu ali otetedzeka, chonsecho, kukhala ndi chilamulo sichipereka chitsimikidzo choti munthu ukukhala mu chilamulo. Ngakhale kuti munthu wakhala okhulupilira kwa nthawi yaitali, kapena kudziwa Mau kwambiri, sizitanthaudza kuti iwe umakhala mu Mau. Umboni oona wachikhulupiliro suli muchidziwitso chomwe munthu wapedza, koma kumvera komwe munthu akukhalamo.

2. Kusiyana Kwa Chiphunzitso Ndi Kuchita Mosayenera
Mtumwi Paulo anaonetsera poyera machitidwe Ayuda mwachinsinsi mu madera atatu pamene amaphunzitsa, “Musabe” uku ndiko kudzipedzera chuma koma munjira yopanda chilungamo, komanso kunena kuti, “musachite Chigololo” ali ozazidwa ndi dama, ndipo “musapembedze mafano” chonsecho osalemekedza nsembe yoyera yoyenera kuperekedwa kwa Mulungu. Chonsecho anaima kwambiri okoledwa mu kuchotsedwa kwa chitetedzo. Chifukwa chomwe chidzudzulo ichi chimamveka mowawa lero ndi chakuti m’chitidwe oyenda m’machimo uwu ndi omwe tikhukhalira m’moyo wathu lero. Chifukwa cha uchimo omwe tikuchita pamene ife tikuphunzitsa ena zomwezo, uku ndi kulakwira kwakukulu kwambiri.

3. Phunziro Lochokera Mukulephera
Pamene moyo wamunthu okhulupilira utsutsana ndi Mau, zotsatira zake sizikhudza munthu m’modzi yekha, chifukwa cha ife, omwe tikuyenera kulemekedza dzina la Mulungu – dzina lomwelo likunyadzitsidwa kwa osakhulupilira. Ngati watsimikidzira kuti uli okhulupilira koma kumakhala moyo osasiyana ndi dziko lapansi, anthu mosakaikira konse ayenera kunyazitsa ndi kunenera mwano Mulungu. Miyoyo yathu payokha ili mboni yokhulupirika ya Ambuye. Tiyeni tsono moona mtima tilape mayendedwe athu akale, ndi kudalira kwatuthu pa Yesu Kristu, ndi kukonzedwanso kukhala molingana ndi Mau.

Abusa Sung – Hyun Kim

Lachiwiri 22, 2026 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Aphunzitsi a Chilamulo Omwe Amaswa Chilamulo
Aroma 2:21-24
Abusa Sung-Hyun Kim