KHALIDWE LA OCHIMWA

(Aroma 3:11-12)


Tikadzindikira chomwe ife tili, chikondi cha Mulungu chimakhala chopambana koposa zonse pa moyo wathu. Sitingathe kumuthangatira koma, “Ichi ndi chopambana kwa Iye.” “Ochimwa anayenera chilango chamuyaya ,” – uku ndiko kunena za choipa choonetsera kuipa mtima kwa munthu. Baibulo linayamba ndikunene kuti, Palibe ngakahale mmodzi olungama ichi chitsimikidzira kuti pali mulandu oti munthu ayankhe ndithu.

1. Kulephera Kumvesetsa
Anthu ali ambuli kwakukulu muuzimu – timatha kupedza chidziwitso cha Mulungu, koma sititha kumvesetsa zapamtima Pake chifukwa cha chikhalidwe cha tchimo chomwe chili pa ife.  Pakusatira zokhumba za thupi, munthu kwa nthawi yaitali wakhala akukana kudziwa Mulungu, mapeto ake – mitima yathu yadetsedwa ndipo chikumbumtima cha uzimu chinadzilala. Monga wakhate yemwe khungu lake silimva ululu, tafika poti sitingalandire chilichonse chochokera kwa Mulungu, ngakhale chikumbumtima chomwe Iye anaika pa ife sichingagwire ntchito monga momwe kunaikidwira.

2. Kulemphera Kufuna Mulungu
Ngakhale kuti munthu ali ndi changu pa zauzimu chachikulu, koma chili chabe ngati zonse tichita pamene tikudzikanidza kwa Mulungu. Sitikumufuna Iye, Koma chonsecho Mulungu anadzifikitsa kale Yekha kwa ife. Yemwe akusaka Mulungu moona mtima amachita zomwe Iye afuna. Munthu otere ndi amene amaika mtima wake kusogoleredwa ndi Mulungu, amabvomeredza kuti ndi wamphamvuzonse, ndipo amapanga chisankho m’moyo wake kukhala mu Mau a Mulungu. Palibe munthu yemwe ali ndi kuthekera kochita izi ndi mphamvu yakuthupi, koma ndi mphamvu ya Mzimu Woyera ndizotheka.

3. Kupatuka Ku Chilungamo
China chotikhadzikitsa pa chiopsyedzo choipa chachikulu ndi kumusiya Mulungu kuti atilore kuyenda monga mwa ntchito zokomera moyo wanthu monga mwa zisankho zathu. Tapatuka ku chilungamo, malingaliro athu nthawi zonse alunjika ku chionongeko – kwa anthu otere, Mulungu anasegula njira ina ndi machitidwe achilendo. Omwe ayenda m’menemo amatchulidwa kuti ndi Akristu. Kukhala Kristu ndiye kuti njira zathu zakale zasandulidzika kwatunthu. Kuyenda munjira iyi zisowekera kukhulupirika ndi kudzipereka kwatunthu. Kutanthaudza kuti kukhadzikika pa Tchalichi mosweka mtima. Kotero kuti sitingayende munjira iyi mosogodzedwa ndi mphamvu zathu za thupi. Ambuye amakhala nafe pa njira yathu yonse. Iyi ndi njira yomwe itilondolera mu Ufumu Wake. Ndipo Mulungu analolera anthu omwe anayendapo kale motsutsana ndi Iye kuyendamo.

Abusa Sung – Hyun Kim

Meyi 3, 2026 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Chikhalidwe Chauchimo cha Anthu: Palibe Amene Amafunafuna Mulungu
Aroma 3:11-12
Abusa Sung-Hyun Kim