Kulemekeza Makolo

(Aefeso 6:2-3)


Mwa magome a miyala omwe Mose analandira, limodzi la ilo panalembedwa za Malamulo a ubale wathu ndi Mulungu, ndipo linalo za ubale pakati pa anthu. Chopatsa chidwi ndi chakuti lamulo lokamba zolemekeza makolo linalembedwa mu magome onse awiri pa Malamulo okhudza ubale wathu ndi Mulungu.

1. Kulemekeza nkhalapakati
“Lemekeza makolo ako,” Lamulo ili limatengedwa ngati limodzi mwa malamulo okhudza ubale wathu ndi Mulungu. Mu ufumu wa Mulungu, makolo ndi nkhalapakati otumizidwa ndi Mulungu. Mulungu anawadalira ndi ulamuliro kukwanilitsa lonjezo la Mulungu kwa ana ao ndi kuwaphunzitsa mau omwe adzasunge kuti akwanilitsidwe. Mwaichi, kulemekeza makolo kuli chimodzimodzi ngati kulemekeza Mulungu.

2. Tsiku lomwe Ambuye adzabweranso
Ndi udindo wa makolo kuphunzitsa ana kulemekeza makolo ao. Ndipo akachita ichi moyenera, sizichitira ubwino iwo okha ayi. Kuphunzitsa ana kulemekeza makolo amakhala maziko odzetsa mtendere pakati pa anthu onse. Omwe aphunzitsidwa bwino m’chitidwe uwu amakhala ndi moyo olemekeza akulu komanso kulemekeza ufulu wa anthu omwe akugwira nao ntchito zina. Kudzichepetsa komanso kukhala adindo komwe aphunzira m’makomo ao zimawathandizira kukhala olemekeza ma ulamuliro komanso kumanga ma ubale abwino ndi anthu onse – malo onse monga pomwe akugwira ntchito za tsiku ndi tsiku komanso malo omwe amapemphera.

3. M’dalitso okoma pa dziko lapansi
“Lemekeza makolo ako, kuti kukhale bwino ndi iwe, ndipo udzakhala ndi moyo masiiku ambiri pa dziko lapansi.” (AEFESO 6: 2-3) Kukoma kwa moyo pa dziko lapansi – ngakhalenso kutalika kwa matsiku amoyo – kwalonjezedwa kwa iwo omwe amvera lamulo ili. Lonjezo ili linatipatsa chilimbikitso chakuti, ngakhale mkati mwa zovuta, timakhala mu chitetedzo cha Mulungu. Ndipo nthawi ndi nthawi, monga ndi nyengo ikhalira, timafika poona mkono wa Mulungu wathu wokhulupirika. Cholowa cha kulemekeza makolo sikuti phindu lake lili mu moyo uli kudza okhawo ayi, ndi mbali imodzi ya m’dalitso omwe tili nao pano ndi lero. Mwa ichi, m’dalitso uwu mwaulemelero ubvumbulutsidwe m’moyo wathu, tiyeni tisunge lamulo loyamba ili lokhala nao lonjezo.

Abusa Sung-Hyun Kim 

Epulo 27, 2025 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Ulemu kwa Makolo ndi Lamulo Loyamba lokhala ndi Lonjezo
Aefeso 6:2-3
Abusa Sung-Hyun Kim