KUUKA KWA AKUFA

(1 Akorinto 15:20-26)


Kuuka kwa akufa sichinthu cha ku uzimu kokha, Mulungu akupulumutsanso matupi athu. Kuuka kwa Kristu ndi chotsimikidzira chipatso choyamba cholalikira za zokolola, ndi mtengo wake oyenera wofikitsa kukhutira pa pangano – kumangiliridwa mu chipulumutso cha Mulungu cholonjedza chomwe chidzalipiridwa mwamphumphu. Popedza Kristu odzutsidwa analandiridwa – kubvomeredzedwa ndi Atate, kuukisidwa kwathu kukuyembekedzera kukwanilitsidwa monga kunaikidwa.

1. Kulowa Kumwamba Muthupi
Anthu ambiri amaganidzira kuti mizimu yopulumutsidwa imauluka kumwamba ngati mzukwa. Koma timapita kumwamba monga munthu wamphumphu – mu thupi. Uku ndiye kuukitsidwa kwa olungama, kuuka koyamba. Mizimu ya awo anapita patsogolo pathu ili ndi Ambuye ngakhale lero. Pamene Malemba akuwanena kuti, “omwe ali kugona,” uku ndi kuyankhula mwaulemu kunena za akufa – palibenso kuwonjedzerapo. Chomwe chidzadzutsidwa pa tsiku lomalidza ndi matupi athu. Patsiku ili, tidzakomananso, maso ndi maso ku thupi.

2. Omwe Akugona Mwa Ambuye
Kodi oyera mtima omwe anachoka ku dziko lapansi ali kuti? Ali ndi Ambuye (2 AKORINTO 5:8) Paulo amawatchula iwo, “omwe ali kugona” – osati kuganizira ngati umo akhalira okomoka, koma njira yapadera  yonenera za imfa. Ichi ndi choonadi chomwe Tchalichi chagwira komanso kubvomeledza kwa zaka zikwi ziwiri. Chifukwa mizimu inapangidwiratu kukhala moyo pa nthawi tinakhulupilira mwa Yesu, ilibenso kusoweka kuti ikaukitsidwenso kachikena. Ndi matupi athu omwe akuyembekedzera kuukitsidwa pa tsiku lomalidza. Ndipo pamene tsiku ili lidzafika, tidzakomana wina ndi mzake kachikena – wamphumphu – ndipo mu thupi.

3. Chigonjetso Choperekedweratu : Kudzikonzekeretsa Komalidza
Kristu adzabwera ku dziko lino lapansi ngati Mfumu – ndi kudzamenya nkhondo yomalidza kutsutsana ndi chinyengo chonse chopandukira, chisalungamo ndi imfa. Adzalamulira mpaka mdani aliyense ataikidwa pansi pa mapadzi Ake – izi zikutanthauza ndi imfa yomwe – mdani omalidza – adzathedwa. Koma chipambano chamtengo wapatali chinaperekedwa kale – chinapambanidwa pa kavali. Uyu yemwe dziko linamukana ndi kumutaya anabweranso – naphwanya mphamvu ya imfa. Mphamvu yomwe inagonjetsa mdima, tchimo ndi imfa lero ili mwa ife. Ndipo pamene Iye adzalamulira – tidzalamulira pamodzi ndi Iye.

Abusa Sung – Hyun Kim

Epulo 5, 2026 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Zipatso Zoyamba za Kuuka kwa Akufa
1 Akorinto 15:20-26
Abusa Sung-Hyun Kim