MULUNGU NDI OKHULUPIRIKA
(Aroma 3:1-3)
Ngati malonjedzo a Mulungu sakukwanilitsidwa – ichi sichifukwa choti Mulungu walephera kukwanilitsa Mau Ake kapena kuti ndi osakhulupirika. Ali Mulungu yemweyo anatitsimikidzira poyera kukhulupirika Kwake pakupereka nsembe Mwana wake yekhayo wokondedwa kutsimikidzira kusunga Mau. Tisanasinkhesinkhe za kusakhulupirika Kwake choyamba tiyenera kudziungudza tokha.
1. Kukonderedwa Kumatsimikidziridwa Ndi Udindo
Israyeri analandira kukonderedwa koposa mosayerekedza mumbiri ya munthu. Mulungu anapangana pagano ndi mtundu uwu basi. Kukhulupilira Malemba pa iwo monga Mau Wopatulika, ndi kulonjedza kutumidza Mpulumutsi kudzera mu fuko lawo. Koma iwo anagwilidzitsa pangano la m’dalitso koma napanga maso awo kukhala akhungu pa undindo ndi zowayeneredza iwo kulandira zolonjezedwazo. Anataya Buku la Chilamulo koma sanadzindikira ichi, anakokeredwa ku njira ya chisalungamo kufikira kuti ngakhale Mpulumutsi anaima pakati pawo koma iwo sanathe kumudzindikira.
2. Chikhulupiliro Chimasowekera Kumvera
Sitiona machitidwe awa mwaife? Tilipo lero pamene Mau akulalikidwa, ena timalandira zina zomwe zikusangalatsa mitima yathu koma zina osadzibvomeredza. Kukhala opita ku Chalichi chaka ndi chaka, kukhala andindo, opedzeka malo a mapemphero nthawi zonse – koma chonsecho mitima yathu ili kutali ndi Mulungu – izi zili chimodzimodzi ndi umo analepherera Israyeri. Popanda kulapa kuchokera pansi pa mtima ndi kusamvera mosogodzedwa ndi machitidwe a chipembedzo chapamaso, Malonjedzo a Mulungu sadzakwanilitsidwa pa ife.
3. Lonjedzo Limabala Chipatso
Malonjedzo a Mulungu akhadzikika pa madera awiri. Malonjedzo omwe anaperekedwa pa Israyeri ngati dziko anakwanilitsidwa ndithu. Ichi sichitanthaudza kuti anthu onse a dzikolo analandira cholowa chawo chifukwa cha chikhulupiliro ndi kumvera kwawo. Malemba akutichenjedza, kuti kuchita ndi Mau a Mulungu mosasamala ndi kusakhulupilira, ndi chikhulupiliro chopanda kumvera chotsogolera ku chionongeko. Mulungu Yemwe sanadzikanidze Mwana wake akuyembekedzerabe ife. Pamene tafika kwa Iye ndi mitima yolapadi ndi yomvera – malonjedzo ake adzabala zipatso zochuluka mu miyoyo yathu.
Abusa Sung – Hyun Kim
Epulo 12, 2026 Utumiki wa Tsiku la Ambuye
Ubwino wa Ayuda ndi Kukhulupirika kwa Mulungu
Aroma 3:1-3
Abusa Sung-Hyun Kim



